Chichewa

Zaka 18 kwa mphunzitsi wochimwitsa mwana

Listen to this article

 

Mphunzitsi yemwe adachimwitsa mtsikana wasukulu wa zaka zosadutsa 16 komanso kumupatsa mankhwala ochotsera pathupi wapukusa mutu wopanda nyanga bwalo la milandu la majisitireti ku Mzuzu litagamula kuti akalangidwe kundende kwa zaka 18.

Apa nkutitu m’bwaloli muli ziii pomwe majisitireti Gladys Gondwe amapereka chigamulo chake kwa Mtendere Phiri, wa zaka 31, wochokera ku Bembeke, T/A Kachindamoto m’boma la Dedza, yemwe amaphunzitsa pasukulu ina ya pulaimale ku Ekwendeni m’boma la Mzimba.

Zidaonekeratu kuti mphunzitsiyu sadali wokonzeka kuti alandira chigamulo cha mtunduwu chifukwa majisitiretiyu asadafike m’bwaloli, Phiri adamveka akufunsa apolisi omwe adali kumuyang’anira ngati zingatheke kutuluka patsikuli.arrest

 

Apolisiwo adamuyankha momupatsa chikhulupiriro chonse kuti zikuoneka kuti zimuyendera ndipo akonzeke chifukwa “patsikuli akagona pofewa kunyumba”.

Komatu zinthu sizidamuyendere chifukwa m’mphindi zisanu zokha, majisitireti adali atapereka chigamulochi. Phiri adangoti zyoli m’chitokosi cha bwaloli.

Popereka chigamulo chake Lolemba, Gondwe adati Phiri akuyenera kuseweza zaka 16 ndi kugwira ntchito yakalavula gaga pogona ndi mtsikana wosakwana zaka 16, ndipo pamlandu wopereka mankhwala ochotsetsa mimba adampatsa zaka ziwiri zomwe ziyendere limodzi ndi za mlandu woyambawu.

Iye adati wapereka chilango chokhwimachi pofuna kupereka phunziro kwa aphunzitsi ena omwe ali ndi khalidwe logonana ndi ana awo asukulu mmalo mowalimbikitsa pamaphunziro awo.

Gondwe adati ngakhale omuimira pamlandu wake Christon Ghambi adapempha bwalolo kuti lisamupatse chilango chokhwima chifukwa nkoyamba kupalamula komanso dziko lino lili pamtsutso wofuna kuchotsa malamulo oletsa kuchotsa mimba, Phiri akufunika chilango chokhwima. n

Related Articles

Back to top button
Translate »