Nkhani

Zaka 50 zaufulu

Ngakhale mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika akuti dziko la Malawi likuyenera kusangalala pa zomwe lakwanitsa m’zaka 50 za ufulu wodzilamulira, akatswiri ena kudzanso mafumu akuti zifukwa zosangalalira sizikuonekabe poyerekeza kuchuluka kwa zaka.

Pamwambo wosangalalira ufuluwu Lamulungu lapitalo, Mutharika adati mwa zina kale dziko lino lidali ndi msewu wa phula wotalika ndi makilomita 96 koma tsopano lili ndi msewu wa makilomita 3200 zokwanira kusangalala.

Ngakhale patha zaka 50 zodzilamulira, sukulu zina zikuoneka ngati iyi
Ngakhale patha zaka 50 zodzilamulira, sukulu zina zikuoneka ngati iyi

“Tili ndi sukulu za ukachenjede zambiri, tikukwanitsa kupeza chakudya chodyetsa anthu oposa 14 miliyoni pomwe kale kudali anthu ochepa. Tiyeni tisangalale zomwe takwanitsazi,” adatero Mutharika.

Koma T/A Kabunduli ya m’boma la Nkhata Bay ikuti zifukwa zosangalala sizikukwanira.

“Kuti ndikambe za boma langali ndiye palibe tingaloze. Chitsanzo, boma langa lili ndi sukulu za sekondale 5 koma palibe ngakhale imodzi yogonera komweko. Kukamba za misewu ndiye yambiri yawonongeka. Msewu wa Chikangawa kuchokera pa Mazamba mukamapita ku nkhalango msewu wake malodza enieni,” adatero Kabunduli.

Senior Chief Nthache ya ku Mwanza ikutinso umphawi wateketa anthu akumudzi zomwe nzovuta kuti angasangalale.

“Kalelo kudali nkhondo, mtendere kudalibe. Pano izi kulibe koma taonani anthu ake, umphawi ndiwosakamba chifukwa anthu akudalirame chimanga ndipo nthaka yaguga,” adatero Nthache.

Iye adadzudzula atsogoleri a ndale posakaza chuma.

“Tikulandira ndalama zambiri m’dziko muno koma sizikupindulira anthu akumudzi, kwachuluka nkuphangira,” adatero iye.

Koma Henry Kachaje, yemwe amakonda kukambapo pankhani zopititsa chuma patsogolo ndi kadaulo pa chitukuko Henry Chingaipe akuti zifukwa zoti Amalawi angasangalale zilipo koma nzochepa poyerekeza ndi zabwino.

Chingaipe yemwenso ndi mphunzitsi ku University of Malawi akuti pa zaka 50 Malawi wakhwima pandale komanso kumanga zinthu zowoneka ngakhale zambiri zidachitika nthawi ya ulamuliro wachipani chimodzi.

Iye akutinso ufulu wachibadwidwe komanso kukhala ndi mabungwe ambiri omenyera ufuluwu ndi chinanso chomwe dziko lino lachita.

“Koma kusangalala kungavute chifukwa umphawi wafika pena. Chitsanzo, banja lililonse likupeza $320 (K128 000) pachaka yomwe ndiyochepa. Dziko lino lili pa 160 pa maiko 182 amene akutukuka kumene. Anthu amene akupeza chakudya chokwanira patsiku ndiwochepa. Kumbali ya maphunziro, Amalawi ambiri pafupifupi 74 pa 100 aliwonse awatu ndiwoyambira zaka 15 kukwera ndiwosaphunzira,” akutero Chingaipe.

“Pano tikudalirabe thandizo la mayiko akunja ndi 41 pa 100 iliyonse,” adaonjeza.

Iye adati dziko lino silikusintha monga maiko oyandikana nawo chifukwa za ziphuphu zomwe zidakula mu 1994 komanso akuti vuto ndiloti lidazindikira mochedwa njira zomwe zingamapereke ndalama kudziko lino.

Koma Kachaje, yemwe ndi mwini wake wa kampani ya Business Consult Africa, akuti n’zachisoni kuti pa zaka 50, dziko lino likusowekabe madzi ngakhale lili ndi nyanja yaikulu komanso mitsinje.

Iye akuti mfundo za atsogoleri asanu amene akhala akulamulira dziko lino chitengere ufulu ndizo zidachititsa kuti dziko lino lisatukuke monga ena akhala akuyembekezera.

“Ndalama yathu idali ya mphamvu koma pano ndi mavuto enieni. Mu 1980 ndalama yathu idali ndi mphamvu, 1 dollar imasintha 80 tambala ya dziko lino. Mu 1992, 1 dollar timasintha K40 koma mu 2004 idatsika mpaka timasintha K100. Pano ndiye sizili mwa kanthu,” adatero Kachaje.

Pa atsogoleri onse, Kachaje adati Kamuzu ndiye adachita zakupsa omutsatira: Bakili Muluzi, Bingu wa Mutharika ndi Joyce Banda. Padakali pano, Peter Mutharika ndiye akulamula.

Malawi adalandira ufulu wodzilamulira kuchoka kwa atsamunda a Chingerezi pa 6 July 1964.

Related Articles

Back to top button