Chichewa

Zaka zinayi kwa ofuna kuba alubino

Listen to this article

Njonda ziwiri zochokera m’boma la Mzimba Lachitatu zidagamulidwa kukasewenza jere kwa zaka zinayi ndi kugwira ntchito yakalavula gaga chifukwa chofuna kuba ndi cholinga chopha mwana wa chialubino wa zaka zinayi wa mwamuna.

Lusungu Sele wa zaka 30 ndipo amachokera m’mudzi mwa Mkoko, T/A Chindi ndi Jailosi Luwanda wa zaka 24, wochokera m’mudzi mwa Vakalani kwa Senior Chief Mtwalo adanyengerera bambo womupeza wa mwanayo kuti amube pamtengo wa K20 miliyoni.

arrest

Koma bwalo la milandu la Mzuzu pa 21 Decemberlidamasula bamboyo, Christopher Kumwenda wa zaka 38 yemwe amachokera m’mudzi mwa Kumwenda, T/A Mzikubola m’boma la Mzimba, ati popeza padalibe umboni wokwanira woti adali ndi cholinga chogulitsa mwana wake womupezayu.

Apa nkhaniyi idatsalira Sele ndi Luwanda.

Ndipo wapolisi woimira boma pamilandu Lloyd Magweje adauza bwalolo kuti Sele adalumikizana ndi Luwanda yemwe amakhala ku Mzuzu kuti ndiye adzagule mwanayo ‘diluyo’ ikatheka.

Bwaloli lidamva kuti mphepo za chiwembuchi zitamupeza mayiyo adathawitsa mwana wakeyu kupita naye m’mudzi mwa Chisewe, m’boma lomwelo.

Koma pa 25 August chaka chatha, Sele adatsatira mwanayu m’mudzimu pomwe adali kusewera pagulu la anzake.

Apa ‘diluyo’ idapheduka popeza Sele adayamba wafunsa wachibale wa mwanayo za momwe angamupezere; ndipo wachibaleyu adakatsina khutu mayi wa mwanayo yemwe adakanena kupolisi kuti akusakidwa.

Ndipo Magweje adapempha bwaloli kuti liwapatse awiriwa chilango chokhwima chifukwa milandu yotere ikuchulukira komanso mwanayo adasiya kusewera ndi anzake ndipo amatsekeredwa m’nyumba.

Podandaula, Sele adauza bwalolo kuti limupatse chilango chozizira poti amasamala banja lake pamene Luwanda adati ndi wamasiye komanso amasamala mkazi ndi ana ake awiri.

Poweruza, majisitileti Tedious Masoamphambe adati chilango chomwe abwalo amayenera kupereka chimafunika chikhale choti anthu akhutitsidwe nacho kuti chithandiza kuteteza ma alubino omwe akuphedwa ndi kuchitidwa nkhanza.

Masoamphambe adati komabe chilangochi chimafunika chikhale chogwirizana ndi mlandu kuti anthu asaganize kuti awiriwa alangidwa mwankhanza.

“Ndili ndi chikhulupiliro kuti chilangochi chiwasintha kukhala nzika zabwino,” Masoamphambe adatero asadapereke chigamulocho.

Koma chigamulochi sichidasangalatse bungwe loona za ufulu wa alubino la Association of People with Albinism in Malawi.

Mtsogoleri wa bungweli Bonface Massa adati akadakonda akadapatsidwa zaka zosachepera 14.

“Nkhaniyo tiiunikanso chifukwa uwu ndi mlandu wofuna kupha munthu umene; nanga munthu wofuna kupha munthu angampatse chigamulo chochepa choncho?” adadabwa Massa. n

Related Articles

Back to top button