Chichewa

Zampira zenizeni ndi CJ Banda

Listen to this article

 

John CJ Banda ndi kaputeni wa Blue Eagles, komanso ndi katundu wofunika ku Flames. Iye wapeza mwayi wokasewera ku Jomo Cosmos m’dziko la South Africa. Kodi apita liti? Nanga mbiri yake ndi yotani? BOBBY KABANGO akucheza naye.

Dzina lonse ndi ndani?

Banda: Amanditcha CJ
Banda: Amanditcha CJ

Dzina langa ndi John Banda koma ondikonda amati John CJ Banda.

Okukonda ake ati? Nanga CJ akutanthauzanji?

Anthu a kwathu ku Nkhata Bay ndiwo adandipatsa dzina la CJ, chidule cha Christopher John Banda amene ankasewera mu Big Bullets. Ati timasewera mpira wofanana. Ena amaganiza kuti adali bambo anga koma ayi, padalibenso chibale ndi ine.

Tamva kuti ukupita ku South Africa, unyamuka liti?

Ulendo mwina ulipo kapenanso ayi. Izi zili chonchi chifukwa eni akewo adamaliza nambala ya osewera akunja amene amayenera alembe komanso nkhani yeniyeni yomwe ndikudziwa ine ndi yakuti sadamalize kupereka ndalama kutimu yanga yomwe adagulira Micium Mhone. Koma zonse zikatheka ndiye mu May muno tipitako komanso dziwani kuti pali matimu ena amene akundifuna ngakhale matimuwo sindingawatchule maina awo pano.

Koma mayeso mudakhozadi?

Kwambiri, ngakhale mutafunsa eni timu akuuzani kuti zidatheka, ntchito tidagwira.

Tandiuzako za chiyambi chako pa chikopa.

Ndidayamba kusewera mpira ku Eagle Strikers mu 2008. Tidali osewera amene tidailowetsa muligi ndipo idatha chaka osatuluka. Mu 2010 ndidachokako ulendo ku Police Training School. Kuchoka uko ndi pomwe ndimadzayamba kusewera mu Blue Eagles. Tidawina Standard Bank Cup mu 2011, Carlsberg Cup mu 2012 ndi Fama Cup mu 2012.

Nanga mbiri yako ku Flames?

Ndidatengedwa kukasewerera Flames mu 2011 pamene timamenya ndi Kenya. Ndasewera magemu 46 ndipo ndachinya zigoli 10, chaka chathachi ndidachinya zigoli zinayi kuposa osewera aliyense mu Flames. Koma ndimasewera pakati.

Uli pabanja?

Mkazi uyo akumvayo, dzina lake Jane komanso mwana alipo dzina lake Sean.

Kodi udindo wako ndi wotani ku polisiko?

Ndine Inspector kulikulu la polisi ku Area 30.

Kodi wina akakugwetsa posewera mpira, sumafuna utangomumanga?

Hahaha! Ayi, ndimadziwa ntchito yanga. Amene aja ndi masewero, komangana ndiye ndi kuofesi. n

Related Articles

Back to top button
Translate »