ChichewaEditors Pick

Zasokonekera ku kapitolo

 

Zili kukapitolo ku Lilongwe si ndizo. Pomwe apolisi achilimika kugwira ndi kutsekera galimoto zopezeka ndi milandu, oyendetsa minibasi agangalama ndipo anenetsa kuti zikaonjeza, apanga zionetsero zosonyeza mkwiyo wawo.

Sabata yatha yokhayi kuyambira Lolemba kufinka Lachitatu kudali mulu wa galimoto kulikulu la polisi mumzindawu ku Area 3 ndipo chiwerengero cha minibasi zokha chimaposa 300.

Nantindi wa oyendetsa basi ndi otolera ndalama udalinso komweko Lachiwiri pomwe Msangulutso udakazungulirako, mkwiyo utalemba tsinya pamphumi zawo kusonyeza kusakondwa ndi zomwe zikuchitikazo.

Ena mwa minibasi omwe adatsekeredwa kupolisi ya ku Area 3
Ena mwa minibasi omwe adatsekeredwa kupolisi ya ku Area 3

Madiraiva ena adati samamvetsa chomwe adagwidwira ndipo adati ngati zotere zingapitirire, nawo aona njira zawo.

“Taganizani munthu kukugwira mmawa mpaka pano 2 koloko akukana kuti ulipire uzipita kokapanga bizinesi. Mmesa munthu akakugwira umayenera kulipira mlandu wako ndi kukuuza zoti ukachite usadabwerere pamsewu?” adatero mmodzi mwa oyendetsa basizo, Valeson Gilbert.

Mosatsutsa kuti akusungadi basizo ndi galimoto zina, apolisi adati akuchita izi ngati njira imodzi yofuna kuchepetsa ngozi mumzindawu panyengo ino ya zisangalalo za Khrisimasi ndi Nyuwere.

Mneneri wa apolisi m’chigawochi, Ramsey Mushani, adati apolisi sagona mpaka ataonetsetsa kuti galimoto zokhazo zomwe ndi zoyenera kuyenda pamsewu ndizo zikuyenda komanso kuti galimoto zonyamula anthu monga basi ndi minibasi zikutsata mlingo woyenera wa anthu okwera.

“Mwina anthu akhoza kumaona ngati tikukhomerera anthu wamba, koma ayi. Kuti mufufuze eni basi ndi galimoto zimene tikusunga muona kuti zina eni ake ndi apolisi, asirikali ndi akuluakulu a m’boma.

“Cholinga chathu n’chakuti ngozi zichepe chifukwa nyengo ngati ino anthu amafuna kukokera ndalama za chisangalalo ndiye amatulutsa galimoto iliyonse yabwino ndi yoipa yomwe, zomwe zimachulutsa ngozi pamsewu,” adatero Mushani.

Momwe nthawi imati 6 koloko mmawa Lolemba, apolisi apamsewu adali atafika kale ndipo ataunjika kale basi ndi galimoto zambiri zomwe zidachititsa kuti chiwerengero cha basi chichepe ndipo mtengo wokwerera basi ukwere.

Anthu ambiri tsikuli adachedwa kutchito zawo chifukwa chosowa mayendedwe mpakana ena amasuti awo adakwera malole kuopa kupalamula kuntchito.

Ena mwa anthu omwe adalankhula ndi Msangulutso adati sakudandaula ndi zomwe apolisi akuchitazo chifukwa akuteteza miyoyo yawo koma adadandaula kuti apolisiwo akagwira basi, amatsitsira anthu panjira zomwe zimawasokoneza.

“Ntchitoyi ndi yabwino chifukwa akuteteza ife tomwe koma vuto lili pakuti akagwira basi amatitsitsira panjira poti kupeza basi ina n’kovuta. Zikadakhala bwino akadati azimuuza wa basiyo kuti akatsitse anthu kenako n’kumutenga.

“Tidavutika ife dzulo (Lolemba) timachoka ku Area 49 ndipo adatitsitsira pa Ntandire poti kukwera basi ina n’kovuta chifukwa zimadutsa zodzadza kale mpaka tidachedwa kuntchito,” adatero Moses Chiumia, yemwe amagwira ntchito ku khonsolo ya mzindawu.

Oyendetsa basiwo adatinso pena akumadabwa kuti ulendo umodzi akulipitsidwa kangapo pomwe iwo amadziwa kuti ukalakwa ulendo umodzi nkulipira suyenera kulipiranso pokhapokha ngati wakanyamukanso ulendo wina.

Mchitidwewu wachititsa kuti njira zam’makwalala zomwe anthu ndi njinga zokha zimadutsa, muyambe kuyenda basi ndi galimoto zolakwa kuthawa kugwidwa ndi apolisi.

Izi zadzetsa nkhawa kumakolo kuti basi ndi galimoto zotere zikhoza kuwaphera ana omwe amakhala akusewera m’makwalalamo.

“Njira zomwe akudutsazo n’zoopsa chifukwa makona ake ngosaonekera patali, mulibe zikwangwani komanso ana adazolowera kuseweramo ndiye mwatsoka wina adzati akhote n’kukumana ndi mwana,” adatero Amina Gibson wa ku Area 36 muzindawu.

Milandu yambiri yomwe ikupezeka ndi yoyendetsa galimoto popanda chiphaso, galimoto zopanda mapepala oyendera pamsewu, matayala akutha ndi kunyamula anthu opitirira muyeso wa galimoto.

Sabata ziwiri zapitazo apolisi mumzinda wa Blantyre adachitanso chimodzimodzi moti nakoso kudali pokopoko mpaka madaraiva a minibasi kuchita zionetsero pofuna kuumiriza apolisi kuti awapatse galimoto zawo koma adawabalalitsa ndi utsi wokhetsa msozi.

 

Related Articles

Back to top button