Chichewa

Zefinati Alick: Kadaulo posema ziboliboli

Listen to this article

Aluso ndi onse koma luso losema ziboliboli si lachibwana, limafunika khama komanso munthu wolimba mtima. Pa Golomoti m’boma la Dedza pali malo otchedwa Golomoti Curios Group amene amapanga ndi kugulitsa ziboliboli. Zefinati Alick nthawi zonse amakhala pamalopa kugulitsa katundu wake uku akupanga wina. BOBBY KABANGO adacheza naye za luso lake motere:
Tidziwane wawa…
Ndine Zefinati Alick, ano ndi malo anga koma zones ndikupangira limodzi ndi mkulu wanga amenenso adandiphunzitsa ntchitoyi.

Alick ndi ziboliboli zake
Alick ndi ziboliboli zake

Kodi malo ano adatsekulidwa liti?
Adatsekulidwa mu 2012, koma ineyo ndidayamba kusema ziboliboli mu 1998. Panthawiyo ndinkagwirira ntchitoyi ku Mua kenaka ndinkapangira kunyumba kwanga. Mu 2012 mpamene timatsekula malo ano.
Ndi zinthu ziti mumasema?
Timasema mtundu ulionse wa zinyama womwe munthu akufuna, chifaniziro cha munthu, Mayi Maria, chifaniziro cha anthu amtundu Wachingoni, galimoto ndi zina zambiri zomwe sindingakwanitse kuzitchula.

Mukugwiritsira ntchito mtengo wanji?
Pali mitengo yambiri yomwe anthu amagwiritsira ntchito koma ife timakonda mtengo wa mtumbu.
Mumagwiritsira zida ziti popanga katunduyu?
Mukakadula mtengowo, mumayenera muyambe kusema ndi sompho, chikwanjenso chimafunika, tchizulo, sandpaper, polishi ndi zida zina ndi zina kuti chomwe tikusemacho chioneke bwino.
Kodi chomwe mwanyamulacho n’chiyani? Nanga zimatenga masiku angati kuti ntchito itheke? Mutiuzenso mitengo yake…
Ichi ndi chifaniziro cha nyama ya chipembere. Chimatenga sabata ziwiri mwina osafikanso malinga ndi nthawi yomwe uli nayo kuti chithe. Chimenechi chikugulitsidwa K10 000. Chinachi ndi chifaniziro cha mayi Wachingoni. Ameneyu amatha mofanana ndi chinyamachi bola ukhale ndi nthawi. Mayiyu timagulitsa K15 000.

Mwathandizika bwanji ndi ntchitoyi?
Ndagula nyumba, ndimalipirira ana sukulu komanso feteleza ndimagula kuchokera n’tchitoyi. Ndipezereponso mwayi kuwauza anthu kuti ife timapanga chilichonse chomwe akufuna, komanso momwe akufuna chionekere.

Related Articles

Back to top button
Translate »