Chichewa

‘Zidayambira m’malingaliro’

Listen to this article

 

Mwina tinganene kuti kulimbikira ntchito ndiko kudapangitsa kuti malingaliro omwe Steve Chimenya wa ku Zomba adali nawo asanduke zenizeni ndi kubweretsa chimwemwe m’moyo mwake.

Mnyamatayu akuti amati akakhala payekha, m’mutu mwake munkabwera chithunzithunzi cha msungwana yemwe adali asadamuoneko n’kale lonse kufikira m’chaka cha 2014 pomwe tsiku lina kuofesi yake kudatulukira msungwana wofanana ndi wa m’malingaliro akewo.

Chimenya ndi nthiti yake patsiku laukwati wawo
Chimenya ndi nthiti yake patsiku laukwati wawo

Rachel Jeremiah Sato wa ku Ntcheu yemwe akuti amagwira ntchito kunyumba ya boma adatumidwa kukagwira ntchito komwe Steve ankagwira ntchito ndipo uku n’komwe zonse zidayambira.

“Nditamuona, ndidadzimenya m’mutumu kuganiza kuti kapena malingaliro aja andipezanso nthawi ya ntchito. Kenako ndidamuona akulowa muofesi yanga ndipo ndidakhulupirira kuti sadali malingaliro chabe. Ndidamupatsa moni, iye n’kuyankha,” adatero Steve.

Iye akuti tsikulo adaweruka mosiyana ndi masiku onse moti olo anthu okumana naye tsikulo ankadabwa ndi nkhope yowala yomwe adali nayo.

Iye akuti chiyambi cha chikondi chawo chidali chomwecho mpaka pa 26 September 2015 adachita chinkhoswe kumudzi kwawo kwa Rachel ku Ntcheu ndipo pa 14 November 2015 lidali tsiku la ukwati woyera womwe madyerero ake adachitikira ku Capital Hotel ku Lilongwe.

Rachel akuti iye atangomuona Steve chinthu chidamugunda mumtima ndipo patapita masiku angapo pomwe Steve ankamuuza za chikondi, mumtima mwake adali atamukonda kale ngakhale kuti panthawi yomwe ankangocheza iye sankaonetsera.

Awiriwa akuti amakonda kupemphera ndipo akufuna mizu ya banja lawo lizike kwambiri mumtima wa Chikhrisitu. n

Related Articles

Back to top button
Translate »