Nkhani

Zigamulo zogwirira zikufooketsa

Listen to this article

Sabata yatha inali imodzi mwa sabata yomwe inaika pa mbalambanda kuya kwa nkhani zogwiririra m’dziko muno. Pomwe bambo wina wa zaka 31 ku Zomba adagamulidwa zaka 21 pogwiririra khanda la miyezi inayi, bambo winanso wa zaka 50 ku Dowa adagamulidwa zaka 14 kundende pogwiririra mwana wa zaka 7. Nako ku Balaka bambo wa zaka 35 adapezekanso wolakwa pa mlandu wogwiririra ndi kupereka pathupi kwa mwana wa mchemwali wake wa zaka 15.

Mchitidwe wogwirira ukuoneka kuti ukuchulukira

Komatu omenyera ufulu wa ana sakukhutira ndi zigamulozi.

Desmond Mhango wa bungwe la NGO Coalition on Child Rights adati pali vuto lalikulu pa kagamulidwe ka anthu ogwirira ana ndipo zilango zomwe zikuperekedwa nzochepa komanso nzosapereka mantha kwa ena.

Malingana ndi Mhango mabwalo a milandu akufunika akhale ndi mlingo umodzi wa zigamulozi osati mlandu wofanana koma zigamulo zosiyana.

“Zikumachitika ndi zoti mlandu womwewo kwina apereka zaka 7, kwina zaka 14, palibe mlingo wofanana. Komanso uyu amugamula zaka 21 pogwirira khanda adzatuluka kundende khandali likadali ndi zaka zochepa ndipo akhonzanso kupereka chiopsezo pa moyo wake,” adalongosola Mhango.

Ndipo iye adanenetsa kuti zigamulozi ndi zokhumudwitsa ndipo adati bungwe lake likuunika njira zina monga kukasuma ku mabwalo amilandu akulu ngati sanakhutitsidwe ndi zigamulo.

Iye adati njira inanso ndi yoti mabungwe omenyera ufulu wa ana azikhala abwenzi a khoti pa nthawi ya mlandu kuti mwina zigamulo zizikhala zazikulu zikulu.

“Komanso nthawi zambiri ife a mabungwe timapereka nthawi yaikulu ku milandu ya m’matauni ndi m’mizinda poyerekeza ndi  milandu ya m’madera atali atali monga ku  Chitipa kapena ku Nsanje,” adadandaula motero Mhango.

Related Articles

Back to top button