ChichewaEditors Pick

Zikhulupiriro zina Zisokoneza mdulidwe

Listen to this article

 

Zikhulupiriro zosiyanasiyana zikusokoneza ntchito ya mdulidwe wa abambo womwe unduna wa zaumoyo komanso mabungwe akulimbikitsa, Msangulutso wapeza.

Ku Nsanje, Dowa komanso ku Nkhata Bay ndi maboma ena amene zikhulupirirozi zachititsa kuti abambo asamapite kuchipatala kukalandira mdulidwewu.

Malinga ndi Senior Chief Dzoole ya m’boma la Dowa, anthu ati samvetsa komwe kumapita kachikopa kamene adulako, zomwe zimawapatsa mantha.

“Anthu amaganiza kuti kachikopa kamene akadulako amakakachitira mankhwala. Maganizo awa ndi amene amachititsa anthu kuno kuti asapite kukalandira mdulidwe.

“Komanso anthu okwatira amaganiza kuti pamene akalandira mdulidwe, ndiye kuti akazi awo aziwayenda njomba chifukwa akawadula sangakakhale malo amodzi ndi mkazi wawo, ati panthawi iyi amaganiza kuti mkazi wawo akhoza kuawayenda njomba,” adatero Dzoole.

Mdulidwe wa abambo wakuchipatala ndi njira imodzi yothandiza kupewa kufala kwa HIV
Mdulidwe wa abambo wakuchipatala ndi njira imodzi yothandiza kupewa kufala kwa HIV

Dzoole adati m’dera lake, mwa amuna 10, amuna anayi okha ndi amene amalandira mdulidwe.

“Kampeni ili mkati moti mafumufe atiphunzitsa kuti timeme anthu akachititse mdulidwe, koma ndi amuna ochepa amene akupita kukalandira mdulidwe,” adatero Dzoole.

Senior Chief Kabunduli wa m’boma la Nkhata Bay wati kampeniyi yakanika kumeneko chifukwa anthu amaganiza kuti akakalandira mdulidwe ndiye kuti alowa chipembedzo cha Chisilamu.

“Ambiri kunoko amaganiza kuti amene alandira mdulidwe ndiye kuti ndi achipembedzo cha Chisilamu. Maganizo amenewa ndi amene akuchititsa kuti anthu asakhale nazo chidwi zokalandira mdulidwezo,” adatero Kabunduli.

Titafunsa mfumuyi ngati ikumemeza anthu ake kuti akachititse mdulidwe, iyo idati: “Ukawauza kuti kachitsitseni mdulidwe, akufunsa ngati iweyo unapanga. Ndiye ine pa msinkhu wangawu sindingapite kumdulidwe.

“Ndinetu munthu wamkulu, ndiye ndikakalandira mdulidwe lero, balalo lidzapola liti? …..sindingapange zimenezo komanso kampeni imeneyi ine sindikuchita nawo.”

Ku Nsanje, malinga ndi McKnowledge Tembo, HIV/Aids co-ordinator pachipatala cha boma, zikhulupiriro za anthu kumeneko zimati munthu akalandira mdulidwe ndiye kuti amaafooka kuchipinda.

“Kunoko tinaphunzitsa mafumu, amipingo ndi azaumoyo za ubwino wa mdulidwe, koma mukamayenda muja, anthu amafunsa zambiri zokhudza zikhulupiriro zawo ndi mdulidwe.

“Palibe amene adabwera poyera kudzatiuza kuti akufooka kuchipinda chifukwa walandira mdulidwe. Komabe anthu upeza akulankhula, ndi zabodza ndipo palibe umboni wake. Zoona zake nzoti macheza amakhalanso bwino m’banja mwamuna akakhala kuti adalandira mdulidwe,” adatero Tembo.

Nayenso Simeon Lijenje wa PSI akuti ndi bodza la mkunkhuniza kuti amuna amene alandira mdulidwe amafooka ndipo wati amuna amene adulidwa ndiwo amachitanso bwino  kuchipinda kusiyana ndi osadulidwa.

“Palibe umboni wa zomwe anthuwo akunena. Dziwani kuti mwamuna amene walandira mdulidwe ndiye amasangalala kuchipinda chifukwa amakwaniritsa bwino chilakolako cha mkazi wake,” adaphera mphongo Lijenje.

Iye adati kampeni ya mdulidwewu idayamba mu 2012 ndipo kuchokera mu October 2014 mpaka September 2015 pafupifupi abambo 93 642 ndiwo alandira mdulidwe m’bomalo.

Achipatala amati ngati abambo alandira mdulidwe, ndiye kuti pali mwayi woti chiwerengero cha anthu otenga kachilombo ka HIV podzera m’kugonana chingachepe ndi anthu 6 mwa 10 alionse (60%), malinga ndi mabungwe a WHO komanso UNAIDS.

Kuyambira mu 2007, mabungwewa akhala akubwekera kuti mdulidwe umathandize kwambiri kuti kachilomboka kasafale kwambiri.

Malinga ndi mabungwewa, maiko 14 a kummwera kwa Afrika komanso kummawa, ndiwo ali kalikiriki kupangitsa kampeni kuti amuna azikalandira mdulidwe.

“Mdulidwe wa abambo ndi pamene achipatala amadula kachikopa kakutsogolo kwa chida cha abambo. Kachikopaka kamasunga zoipa, koma ngati walandira mdulidwe, amakhala waukhondo. Zoipazo zimakhala zasowa malo oti zisungidwenso,” lidatero lipoti la UNAids, nkuonjera kuti mdulidwe umathandiza kuchepetsa matenda a khansa ya khomo la chiberekero cha amayi.

Related Articles

Back to top button