Nkhani

‘Zilango zophweka zivulaza maalubino’

Listen to this article
  • Miyezi 18 kwa ofuna kugulitsa alubino ku DZ

Pali mantha kuti maalubino angapitirire kuona zokhoma m’dziko muno ngati boma silichita machawi kuti lamulo latsopano loteteza anthuwa liyambe kugwira ntchito, mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa maalubino la Association of People with Albinism in Malawi (Apam), Bonface Massah, watero.

Mantha a mkuluyu akudza pamene anthu amene apezeka olakwa pozunza kapena kusowetsa maalubino akupitirira kulandira zilango zozizira.albinos

Lachisanu sabata yatha, bwalo la milandu m’boma la Dedza lidagamula mayi Siyireni Nyata ndi Chrissie Lajabu kukaseweza kundende zaka ziwiri ndi miyezi 6 poopseza mwana wa zaka 14 kuti ‘amupezera kale msika.’

Malinga ndi mneneri wa polisi ku Dedza, Edward Kabango, amayiwa akhala akulankhula izi kwa nthawi yaitali.

“Amati ndi kanyama kosendasenda ndipo akapezera kale msika woti akakagulitse,” adatero Kabango.

Kaamba ka kuopsezedwako, mwanayo akuti adasiya sukulu pochita mantha kuti angakumane ndi anthu amene amati amugulawo. Makolo a mwanayu akuti adakadziwitsa apolisi ndipo pa April 15 amayi awiriwo adanjatidwa.

Bwalo lidawapeza olakwa ndipo lidawaimba mlandu wobweretsa mantha kwa mwanayu ndipo adawalamula kuti akaseweze zaka ziwiri ndi miyezi 6 kundende.

Chilangocho chikudza pamene mkulu winaso ku Machinga, Sinoyo Wyson, wagamulidwa kuti akakhale kundende zaka ziwiri posowetsa mwana wa zaka 11 wachialubino.

Mu May chaka chinonso amuna awiri ku Zomba adawalamula kukaseweza miyezi 12 popezeka ndi mafupa alubino.

Massah akuti si zoona kuti milandu yotere izikhala ndi zilango zofewa ndipo wati bungwe lawo lichitapo kanthu kuti maalubino asamakhale mwamantha.

“Ndikumvanso kwa inu za nkhani ya ku Dedzayo, koma tifufuza. Pankhani ya ku Machinga ndiye tidakagwadanso kubwalo lalikulu kuti aunikenso chilangochi,” adatero Massah.

Koma iye adati oweruza milandu si olakwa pa zigamulo zomwe akuperekazi chifukwa malamulo a dziko lino amapereka zaka ziwiri kwa wopalamula mlandu wozembetsa munthu.

Iye adati mavuto onsewa angathe ngati lamulo la Anti-Human Trafficking lingayambe kugwira ntchito. Lamuloli lidavomerezedwa kale ndi aphungu a Nyumba ya Malamulo komanso mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika.

“Lamulo latsopanoli likupereka zaka khumi kwa amene wapalamula mlandu wonga uwu, chomwe ndi chilango chokhwimirako. Tayesera kufunsa anzathu a boma nthawi yomwe lamuloli liyambe kugwira ntchito koma zomwe tikumva si zopereka chiyembekezo.

“Maalubino sakutetezedwa kupatula kungolankhula chabe, zomwe sizingateteze anthuwa,” adatero Massah.

Koma mneneri muunduna woona za chilungamo ndi malamulo, Apoche Itimu, akuti lamuloli lidavomerezedwa kale ndi Mutharika.

“Chomwe ndikudziwa n’chakuti lamuloli lidavomerezedwa, sindingakumbuke kuti lidasindikizidwa liti. Panopa kwangotsala kuti liyambe kugwira ntchito, koma ngati mukufuna kudziwa zenizeni za lamuloli funsani unduna wa zam’dziko,” adatero Itimu pouza Tamvani.

Mneneri ku unduna wa zam’dziko, Rose Banda, Lachiwiri m’sabatayi adati timuimbire tsikulo lisadathe kuti atipatse zenizeni zokhudza lamuloli.

Koma pakutha pa tsikulo Banda adati sadakumane ndi oyenerera amene angamufotokozere nkhani yonse yokhudza lamuloli.

Lachitatu adatitumizira uthenga pafoni kuti akhala ndi zotsatira zonse pofika Lachinayi.

Maiko monga Tanzania, Mozambique, South Africa ndi Zambia ali ndi lamuloli lomwe limakhaulitsa opezeka kuti apalamula mlanduwu, pamene mtsogoleri wa dziko la Zimbabwe Robert Mugabe adakhazikitsa ndondomeko yapadera yothanirana ndi anthuwa.

Mutharika wakhala akumalankhula pawailesi ya MBC mawu oopseza kuti amene apezeke akusautsa maalubino athana nawo.

Koma ngakhale Mutharika angalankhule maka, kukhoti akuyendera zomwe malamulo amanena posatengera mawu ake. Izi zapangitsa mabungwe monga Apam kuti alimbikitse kupempha boma kuti likhazikitse lamulo lokhwima pofuna kuteteza miyoyo ndi maufulu a maalubino.

Massah akuti nthawi yakwana kuti mabungwe amene amamenyera ufulu wachibadwidwe ndi ena agwirane manja pofuna kuthana ndi mchitidwe wozunza maalubino.

“M’dziko muno mukangochitika nkhani mumaona amabungwe akubwera pamodzi kudzudzulapo, koma zomwe zikuchitika m’makhoti athu palibe amene akulankhulapo. Tikufunika tigwirane manja kulimbana ndi nkhaniyi ngati tikufuna tipambane nkhondo yoteteza anthu [amene ali ndi zilema monga maalubino],” adatero Massah.

Nkhani zosowetsa maalubino komanso kufukula manda awo zidafika pachimake mu February chaka chino ndipo anthuwa pamodzi ndi amabungwe ena adachititsa msonkhano mumzinda wa Blantyre kudandaulira boma kuti lichitepo kanthu.

Pamsonkhanowo, Senior Chief Kawinga ya m’boma la Machinga idati ndi zosamveka kuti chilango cha wosowetsa munthu chizikhala chochepa.

“Munthu wina adaba ng’ombe koma adamupatsa chilango choti akakhale kundende zaka zisanu pamene wosowetsa munthu akumupatsa zaka ziwiri. Pali chilungamo apa? Kodi ng’ombe ikhale yofunikira kwambiri kuposa munthu? Kodi alubino si munthu?” adadandaula Kawinga.

Related Articles

Back to top button
Translate »