Chichewa

Zinthu zitatu mu nkhuku imodzi ya Mikolongwe

Listen to this article

Katswiri wa ulimi wa ziweto wa ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) Timothy Gondwe wati kukhala ndi nkhuku ya Mikolongwe imodzi ndi chimodzimodzi kukhala ndi nkhuku zitatu—yanyama, yachikuda ndi yamazira.

Nkhuku ya Mikolongwe imafika makilogalamu 4.5

Iye adati nkhuku ya Mikolongwe imakula kwambiri, imaikira mazira ambiri, komanso kukoma kwa mazira ndi nyama yake ndi chimodzimodzi nyama ndi mazira a nkhuku yachikuda.

“Nkhuku ya Mikolongwe imakula kwambiri  moti tambala mpaka amafika makilogalamu 4.5 pamene thazi amatha kulemera makilogalamu 4 pa miyezi 4 kapena 6 yokha.

“Pachaka nkhuku ya Mikolongwe imaikira mazira apakati pa 200 ndi 250,” adatero Gondwe.

Kuonjezera apo, katswiriyu adati mlimi atha kukwatitsa anapiye ake ndi a nkhuku zachikuda kuti akhale nkhuku zolimba komanso zopirira ku matenda.

Gondwe adati ichi n’chifukwa chake nkhukuzi zikhoza kuwetedwa kumudzi ndikumabweretsa phindu lochuluka.

Malingana ndi katswiriyu, nkhuku zokwatitsazi zimakula ndi kuikira mazira ambiri oposa azachikuda.

“Mazira ake amaposa a nkhuku zachikuda ndi magawo a pakati pa 20 ndi 30 pa 100 aliwonse ndipo zimatha kuikira okwana 200 pachaka,” iye adatero.

Gondwe adati izi zimathandiza mlimi kupeza nyama yochuluka ndi mazira ambiri choncho ndalama, komanso ndiwo sizisowa pakhomo.

Mlangizi wa ziweto wa ku Blantyre Agriculture Development Division (Bladd) John Pirate Kothowa adati ngakhale nkhukuzi zimakula, komanso kuiikira mazira ochuluka n’zosiyana kwambiri ndi zachikuda m’chikhalidwe chake.

Iye adati ichi n’chifukwa chake zimatha kumayenda  n’kumadzitolera zokha chakudya.

“Chifukwa choti zimatenga nthawi yotalikirapo kuti zikule, kuziweta ngati zachizungu pomazidyetsa chakudya chogula n’kudzichepetsera phindu,” adatero Kothowa.

Gondwe adati alimi akumidzi akhoza kuweta nkhukuzi ngati momwe amawetera  zachikuda, koma zimafunika kumazipatsa chakudya choonjezera  m’mawa, masana ndi madzulo.

Iye adati chakudyachi ndi monga gaga wothira mchere pang’ono ndipo ngati pali zakudya zina za m’gulu la nyemba, azisakanizako gawo limodzi mwa magawo atatu aliwonse.

Katswiriyu adafotokoza kuti mlimi aziika chakudyachi pafupi ndi khola kapena pamene nkhuku zimakonda kudutsapo zikamapita kukadya.

“Pambali pa chakudya pazikhala madzi akumwa aukhondo kuti zizimwa momwe zafunira.

“Mlimi azitsatira dongosolo lonse la katemera wa chitopa kuti zikhale zotetezeka,” iye adatero.

Gondwe adafotokoza kuti khola lizikhala lotakasuka, louma, lolowa bwino mpweya  ndipo ngati n’kotheka la m’mwamba chifukwa ndi lomwe nkhuku zoyendayenda zimakonda.

Katswiriyu adafotokoza kuti alimi am’tauni omwe amatha kupeza mwayi oweta nkhuku zokwatitsa, akhoza kumazipatsa chakudya chopanga okha kapena chogula cha nkhuku za mazira, koma chizingokhala choonjezera chabe.

Iye adati izi zili choncho chifukwa nkhuku za Mikolongwe zimadana ndikutsekeredwa m’khola.

Lastseen Jonamusi ndi m’modzi mwa alimi a nkhuku za Mikolongwe mu mzinda wa Blantyre wayamikira ulimiwu kuti ndi wabwino.

Iye adati adayamba kuweta mu December chaka chatha koma padakali pano zakula kale.

“Pano maso ali kunjira kudikirira tsiku lomwe ziyambe kuikira mazira kuti ndiyambe kudyerera,” adabwekera motere mlimiyu.

Related Articles

Back to top button