Chichewa

Zionetsero ponseponse

Listen to this article

Nyimbo imene idavuta pa Wenela tsiku limenelo idali ya Lucius Banda, Jennifer.

Mundiuzire Jennifer

Ayeayeyeye

Mundiuzire afatse

Ayeayeyeye

Kokafuna maunitsi akatengako Edzi.

Abale anzanga ndiye kudali kuvina ngati tili ku Crossroads Hotel kuyembekezera kudzaonera ukwati woyera pa 20 December pano.

Atabwera Abiti Patuma, adati akudzangonditsanzika chifukwa unali ulendo wautali amati auyambewo.

“Pa Wenela pandilaka. Lero lino ndikupita ku Chitipa, kumene kuli Amalawi enieni a mtima monga Chilembwe. Pamene wapondedwa si bwino kunena kuti akulu mungathe kuchotsako phanzi lanu chifukwa langa lalowa pansi pa phanzi lanulo,” adatero Abiti Patuma.

Palibe chimene ndidatolapo.

“Kumenekotu anthu sakuyesa, akwiya chifukwa kuchipatala akupereka chakudya kamodzi patsiku ngati kundende. Tsono munthu angachire bwanji pamene sakudya? Sakukambatu za kusowa kwa mankhwala,” adatero Abiti Patuma.

Abale anzanga, ndikamati Abiti Patuma amandisokoneza ndimanena chifukwa cha zinthu ngati izi.

Adandiyang’anitsitsa.

“Nchifukwa chake Billy Wayaya akamapita yekha pamsewu kusonyeza mkwiyo palibe amamumvetsa. Umbuli ndi nthenda yoopsa zedi. Pajanso kuli za anamwino kuyenda pamsewu. Za ana asukulu otsekeredwa chifukwa cha zionetsero ndiye sitinganene,” adapitiriza.

Apa ndipo ndidayamba kuzitolera. Paja zionetsero ndiye zangoti mbweee!

“Zisandikhudze. Zidzandikhudza mukadzakonza chionetsero chonena kuti mukufuna Adona Hilida abwerera kuno ku Wenela. Oipa athawa yekha ndi amodzi mwa mawu omwe adandisiyira atate anga,” ndidatero.

“Za Adona Hilida usachite kukamba. Iwotu ali ngati asirikali akuluakulu a ku Germany amene adazunza Ayuda zaka zapitazo. Nkhondoyo itangotha, asirikaliwo adali kuthawa m’dzikolo, ena kukagwidwa ku Brazil mpaka,” adatero Abiti Patuma.

“Ukutanthauza kuti akusiyana ndi Nelson Mandela yemwe adayamba kukhala moyo wothathawa kunja asanakhale paulemerero? Inetu sindikudabwa, chifukwa amabwera ndi zinthu zodabwitsa. Pajatu ndiwo adationetsa kuti n’zotheka otsutsa kubera chisankho! Adationetsanso kuti kusolola mwakathithi n’kotheka ngakhale wina aomberedwepo,” ndidatero.

M’maso mwanga ndimaona mayi wina pompano pa Wenela amene ankakonda kupachika litaka la nsalu paphewa, ati mudzi wonse udziwa palibe ali ndi zitenje zochuluka kuposa iye pano pa Wenela.

Abale anzanga dziko laipa ili, kunjaku kwaopsa zedi.

“Zoona Moya Pete alemba ntchito munthu wosamudziwa polingalira kuti palibenso amadziwa ntchito kuposa iye? Akuluwa phindu lawo ndimalephera kulimvetsa. Pajatu masiku ano kuti upeze ntchito yapamwamba uyenera kudziwana ndi akuluakulu. Palibe cha mahala,” adatero Gervazzio ngati wadzuka kutulo.

Koma imene amayambitsayo akadaikwanitsa?

“Ndiye ndangomva kuti ayamba akana kumulemba ntchitoyo? Koma apa pakuonekanso kuti pavuta. Kapena pakufunika kachionetsero kapadera?” adabwekera Abiti Patuma.

Gwira bango, upita ndi madzi! n

 

 

 

Related Articles

Back to top button