Nkhani

Zionetsero zokhudza achialubino zilipo

Listen to this article

Anthu achialubino anenetsa kuti achitabe m’bindikiro kunyumba ya boma ya Kamuzu Palace mwezi wa mawa pofuna kukakamiza boma kuti lichitepo kanthu pa za kuphedwa kwawo.

Wapampando wa bungwe la Association for People with Albinism in Malawi (Apam) Overstone Kondowe wati m’bindikirowo ulipo kuyambira pa 6 mpaka 8 March, ngakhale nduna ya zachitetezo Nicholas Dausi yapempha anthuwo kuti adekhe kaye chifukwa nkhaniyi siyinafike pochita zionetsero.

Flashback: Massa is seen with a placard during the search for Mark Masambuka who was later found murdered

Malinga ndi Kondowe, anthu adzayenda kuchokera pabwalo la Community m’tauni ya Lilongwe kudzera ku Nyumba ya Malamulo mpaka kunyumba ya boma ya Kamuzu Palace kukapereka kalata kwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika.

Kondowe adati, anthuwa akakhala konko kwa masiku atatu, ndipo masikuwa akakadutsa asadayankhidwe zakupsa akapempha mtsogoleriyu kulengeza kuti dziko lino lino lili pa chiopsezo moti iwo sangakhalemo.

“Tikatero tidzapempha mabungwe ndi maiko akunja kutenga anthu achialubino omwe akusowa chitetezo m’dziko muno kupita m’maiko awo momwe muli chitetezo chokwanira,” adalongosola motero.

Iye adati anthu achialubinowa adzapempha kuchoka m’dziko muno, pokhapokha mtsogoleri wa dziko lino akadzapanda kuwayankha madandaulo awo.

“Mtsogoleriyu akadzapanda kutiyankha, tikupempha aliyense yemwe ndi wa chialubino kudzasonkhana ku maofesi a akazembe oimira maiko akunja m’dziko muno kuti apite ku maiko awo,” adatero Kondowe.

Malinga ndi Kondowe kalata yomwe akukapereka kwa Mutharika ili ndi madandulo akuluakulu asanu.

Mwa madandaulowa ena akupempha boma kuti lipereke ndalama zokwana K3 biliyoni ku ndondomeko zomwe zidakhazikitsidwa chaka chatha momwe muli ntchito zothandizira anthuwa zomwe mwa zina zikukamba zowamangira nyumba zolimba zoti zigawenga zizikanika kuthyola, kuwapatsa chitetezo chokwanira.

Iye adatinso anthuwa akufuna bwalo la milandu la paderadera loweruza milandu ya anthu okhudzidwa ndi kuphedwa kwa anthu achialubino.

“Tikufunanso kuti kukhazikitsidwe bungwe lapadera lofufuza komwe akuti kuli misikako chifukwa ife tikudabwa kuti anthu omwe akugwidwa ndi ang’onoang’ono awa, koma osati akuluakulu awo, eni ndalamawo,” adatero Kondowe.

Iye adati zafikapa boma komanso mtsogoleri wa dziko lino alephera kuwateteza.

Malinga ndi Kondowe dziko lino liunikenso malamulo a ufiti komanso asing’anga azikhala m’kaundula ndi kumagwira ntchito yawo motsatira malamulo okhazikitsidwa.

Koma Dausi adauza msonkhano wa atolankhani Lachiwiri ku Lilongwe kuti anthu a chialubino achepetse moto chifukwa zinthu sizidafike povuta penipeni.

“Zinthu sizidafike poti n’kuabindikira ku nyumba ya chifumu kapena kuyamba kupempha kusamuka m’dziko muno ndi kukakhala kumaiko a kunja,” adatero Dausi.

Izi zawonjezera mkwiyo wa anthuwa omwe pofika Lachitatu bungwelo lidalengeza kuti atuluka munthambi yomwe mtsogoleri wa dzino lino adakhazikitsa poyang’ana za ufulu wa anthuwa.

Kondowe adati zomwe adanena Dausi zikusonyeza kuti boma lilibe chidwi pa chitetezo cha anthu a achi alubino.

Kuchokera m’chaka cha 2014, anthu okwana 25 ndiwo aphedwa m’dziko muno pa zikhukhulupiliro zoti mafupa ndi zina mwa ziwalo zawo n’zolemeretsa.

Ndipo naye womenyera ufulu wa anthu Gift Trapence adati a mabungwe apitiriza kukakamiza boma kuti liteteze anthuwa popereka ndalama ku ndondomeko yomwe muli ntchito zowatetezera chifukwa pakadalipano palibe chomwe bomali likuchitapo.

Iye adatinso ali ndi chisoni chachikulu chifukwa cha kulankhula kopasula kwa Dausi.

“A boma alephera, ndi chifukwa chake anthuwa akufuna kungosamuka m’dziko muno. Ndife okhumudwa kwambiri,” adatero Trapence.

Koma pomwe Tamvani adalankhula ndi mmodzi mwa asing’anga m’dziko muno pofuna kumvetsetsa ngati ziwalo za anthu achialubino zingalemeretse anthu, sing’anga wina wa m’boma l;a Salima Jamitole Kadango adati ndi bodza la mkunkhuniza kuti munthu angalemere ndi ziwalo za anthuwa.

“Zikuchitika kwathu kuno ndi chipongwe chabe, palibe angalemere

chifukwa cha ziwalo za anthu achialubino. Anthuwa akuphedwa chabe. Ife ngati asing’anga kwathu n’kuchiza anthu basi,” adatero Kadango.

Pomwe mfumu Kameme ya m’boma la Chitipa kumalire a dziko lino ndi la Tanzania komwe mchitidwewu udachokera idati zomwe zikuchitika m’dziko muno ndizochititsa manyazi.

“Bwanji boma kufufuza za momwe anzathu a ku Tanzania adathana nalo vutoli? Apa tisalozanenso zala koma tifufuze kuchokera kwa anzathuwa za momwe adachitira,” adatero Kameme.  n

Related Articles

Back to top button