Nkhani

Zipani zigonjera chiletso cha Escom

Listen to this article
Chipani cha MCP chati chichotsa mbendera pamapolo
Chipani cha MCP chati chichotsa mbendera pamapolo

Zipani za ndale m’dziko muno zagwirizana ndi chiletso cha bungwe loyendetsa ntchito za magetsi m’dziko muno la Escom choti zipani zandale zisamapachike mbendera zawo pazipangizo zake monga mapolo a magetsi.

Mneneri wa chipani cha MCP Jessie Kabwila wati bungwe la Escom ndi lolandiridwa paganizo lakeli, koma wapempha kuti bungweli litsate njira zabwino pochotsa mbenderazo kuopa kuononga.

“A Escom sakulakwitsa chifukwa akuganizira za chitetezo cha anthu, koma tingopempha kuti pakhale kulumikizana kwabwino kuti katundu wathuyu asaonongeke poti ndi wodula,” adatero Kabwila.

Mlembi wamkulu wa chipani cha PP Wakuda Kamanga naye wati palibe cholakwika bungwe la Escom kuchita izi chifukwa ngozi za magetsi zimaopsa, makamaka ngati anthu akuseweretsa zida za magetsi.

“Iyi ndi njira imodzi yomwe bungwe la Escom laona kuti ikhoza kuthandiza kuchepetsa ngozi komanso kuteteza katundu wawo, choncho ife tikambirana ndi achinyamata athu kuti akachotse mbendera zomwe zili pamapolo a magetsi,” adatero Kamanga.

Koma mneneri wa chipani cha DPP Nicholas Dausi adati chipani chawo sichipachika mbendera zawo m’mapolo a magetsi.

“Zimenezo mukafunse a PP, ife sitiika mbendera pamapolo a magetsi,” adatero Dausi Tamvani itamufunsa za maganizo a chipani chake pa chiletso cha bungwe la Escom.

Wachiwiri kwa mneneri wa bungwe la Escom George Mituka wati bungweli lidayamba kuganiza za nkhaniyi kalekale ndipo lakhala likukambirana ndi makampani ndi makhonsolo pa chimene angachite.

Mituka adati aganiza zochita izi pano poona mmene mchitidwewu wakulira ndi momwe ngozi zokhudza magetsi zikuchitikira.

“Nkhaniyi tidaiyamba kalekale koma pano taona kuti zanyanya ndiye palibe kuchitira mwina moti pano tayamba kale kuthothola,” adatero weachiwiri kwa mneneri wa bungweli.

Mneneri wa bungwe loyendetsa zisankho m’dziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC), Sangwani Mwafulirwa, wati ndi mlandu kupachika mbendera za chipani m’malo osaloledwa ngakhale kuti malamulo a MEC sanena chilango chomwe wopezeka akutero angalandire.

Bungwe la Escom lidaletsa zipani kupachika mbendera zawo pazipangizo zake maka mapolo a magetsi ndipo lidati lidzathothola mbendera ndi zipangizo zina za kampeni zomwe zidapachikidwa kale.

Bungweli lati kupatula kuti mchitidwewu ndi woopsa, zipangizo zawo zimawonongeka ndipo izi zimasokoneza ntchito zawo.

“Escom sidzakhudzidwa ndi ngozi iliyonse yomwe ingaoneke pomwe anthu akupachika mbendera pamapolo a magetsi, komanso idzaimba mlandu yemwe adzapezeke akupachika mbenderazi pamapolo ake. Ndipo pomaliza Escom ithothola mbendera zonse zomwe zidapachikidwa kale,” chatero chikalata cha Escom.

Koma ngakhale bungwe la Escom lanena kuti layamba kale kuchotsa mbendera ndi zipangizo zina za kampeni m’mapolo a magetsi , mbenderazi zidajali petupetu m’mizinda, m’matauni ndi m’maboma pamene kwatsala mwezi umodzi ndendende kuti chisankho chapatatu chichitike pa 20 May.

Related Articles

Back to top button