Nkhani

Zipani zikufuna machawi pa chisankho

Listen to this article

Zipani zandale zati bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lichititse msanga chisankho chobwereza kudera la kummwera cha ku mmawa kwa Lilongwe kuti anthu akuderari akhale ndi phungu owayimirira ku Nyumba ya Malamulo.

Izi zikutsatira chigamulo cha bwalo lalikulu la apilo kuti chisankho cha phungu wa deralo chichitikenso litaunika dandaulo la yemwe ankayimirira chipani cha Malawi Congress Party (MCP) Ulemu Msungama kuti chisankhocho sichidayende bwino.

Sipikala wa Nyumba ya Malamulo Richard Msowoya watsimikiza kuti kutsatira chigamulochi, deralo tsopano lilibe phungu.

“Bwalo lomwe lagamula ndi lalikulu m’dziko muno kutanthauza kuti kulibenso komwe nkhaniyo ingalowere. Apa, zikutanthauza kuti kuderako kulibe phungu n’chifukwa chake kuchitikenso chisankho,” adatero Msowoya.

Pachisankho cha pa 20 May, 204, bungwe la Mec lidalengeza kuti Bentley Namasasu yemwe ankayimira chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) ndiye adapambana koma Msungama adakamang’ala kubwalo la milandu za chigamulochi.

Wachiwiri kwa mlembi wa chipani cha MCP Eisenhower Mkaka adati bungwe la MEC lisakoke nkhaniyo koma kuthamangitsa chisankhochi kuti anthu a

m’deralo akhale ndi phungu owayimilira ku Nyumba ya Malamulo. Mneneri wa chipani cha People’s Party (PP) Noah  Chimpeni adati MEC  iyambirepotu kusakasaka ndalama zopangitsira chisankhochi mawu omwe adagwirizana ndi a mneneri wa chipani cha UDF Ken Ndanga.

“Apa MEC iyambiretu kusakasaka ndalama zopangitsira chisankhochi munthawi yake kuti ikwaniritse ntchito yake malingana ndi malamulo,” adatero Ndanga.

Chikalata chomwe MEC idatulutsa Lachitatu, chidati pali z ofunika kutsata chisankhochi chisadachitike.

Aka kakhala koyamba kuti chisankho cha mtundu uwu chichitike mumbiri ya Malawi. Motero, tikuyenera kuunika bwino chigamulochi ndi malamulo oyendetsera chisankho kuti akutinji,” chidatero chikalatacho.

Mneneri wa bungwelo Sangwani Mwafulirwa adati malamulo sanena nthawi yeniyeni yofunika kutenga kuti chisankho chotere chichitike ndipo mmalo mwake akhoza kugwiritsa ntchito lamulo lomwe limati pasadathe masiku 60.

Mwafulirwa adatinso mwa zina, bungweri likufunika kuti lisake ndalama zopangitsira chisankhochi chifukwa mundondomeko ya chuma ya 2016 mpaka 2017 mulibe pologalamu yachisankhochi.

Related Articles

Back to top button
Translate »