Nkhani

Zisangalalo zafika, samalani

Nyengo ya zisangalalo za Khrisimasi ndi chaka chatsopano (Nyuwere)  yafika koma apolisi achenjeza kuti onse osangalala mopitiriza muyeso adzakumana ndi zokhoma zomwe sadzaiwala.

Wothandizira mneneri wapolisi m’dziko muno a Felix Misomali ati apolisi akhazikitsa ndondomeko yokhwimitsira chitetezo yomwe siyidaonekeko n’kale lonse panyengoyi.

“Monga mukudziwa kuti boma likusintha kagwiridwe kantchito pofuna kukonza zinthu, nafe kuno kupolisi tikusintha zinthu kuti Amalawi azikonda utumiki wathu powona chitetezo chomwe akulandira,” atero a Misomali

Mu nyengo ngati ino mumachuluka zochitika monga ngozi za pamsewu, anthu kumira pooloka mitsinje yodzadza ataledzera komanso umbava ndi umbanda.

Pofuna kuchepetsa izi m’nyengoyi chaka chino, a Misomali ati apolisi akhazikitsa malo oyang’anira mmene madalaivala akuyendetsera galimoto zawo ochuluka, ndipo kukhala zilango zikuluzikulu.

“Talandira kale makamera oyezera mathamangidwe a galimoto komanso zija zoyezera ngati munthu waledzera ndipo kuli zilango zachindapusa zoyambira K70 000 mpaka K200 000,” atero a Misomali.

Iwo atinso apolisi akuyendera ndikuphunzitsa akabaza onse a njinga zamoto ndi zakapalasa momwe angapewere ngozi popeza ngozi zambiri za pamsewu zikumachitika chifukwa cha akabaza.

Pofuna kuthana ndi umbanda komanso umbava, iwo ati anthu asadabwe akaona apolisi ali paliponse komanso akaona zipata zoonera galimoto malo osayembekezeka.

“Ndi pulani yathu kuti paliponse, kaya n’kumudzi kaya m’tauni, pakhale apolisi ndipo sakhalamo ngati zikwangwani ayi, azigwira ntchito yawo ndiye wina alodzedwe kusokoneza awone,” achenjeza a Misomali.

Iwo aonjeza kuti apolisi osavala yunifolomun akhalanso ali ponseponse.

Poomba mkota wachitetezo chonse, a Misomali ati apolisi akhwimitsanso kwambiri chitetezo cha m’zipata zolowera ndi kutuluka mdziko chifukwa nthawi zina aupandu amatha kuoloka m’malowa n’kudzayambitsa zisokoneza.

Iwo apempha anthu kuti apewe mchitidwe omwe ungapereke danga kwa aumbava ndi mbanda poonetsetsa kuti asiya munthu ozindikira pochoka pakhomo komanso apewe kulengeza zamayendedwe awo mmasamba a mchezo.

“Izi zomangoti mwapita kunyanja basi m’masamba a mchezo mose mbweeee mbava zimachita kudziwa kuti nyumba yanu yatsala yokha ndiye akhoza kukapanga chilichonse,” atero a Misomali.

Iwo apemphanso anthu kuti aziyenda mosamala pamsewu komanso aziyamba awona kaye galimoto asadakwere pochepetsa ngozi za pamsewu.

A Misomali ati pa nyengo ya khrisimasi ndi nyuwere yapitayo, kudachitika ngozi 109 zomwe padafa anthu 23 ndipo milandu ina ngati yothyola ndi kuba idalipo 27.

Iwo ati ngozi ndi umbandawo zidachitika kuchoka usiku wa pa 24 December mpaka usiku wa pa 26 December 2020 komanso usiku wapa 31 December 2020 mpaka usiku wapa 1 January 2021.

Related Articles

Back to top button