Nkhani

Zochitika ku mwambo wa kulamba

Listen to this article

Loweruka lapitalo kudali chaka ku likulu la mfumu yaikulu ya Achewa m’maiko a Malawi, Zambia ndi Mozambique Kalonga Gawa Undi ku Mkaika m’boma la Katete ku Zambia. Khamu la anthu ochokera m’maikowa lidapita kumeneko kukachita nawo mwambo wa Kulamba.

Malinga ndi kufotokoza kwa mkulu wa bungwe la Chewa Heritage Foundation (Chefo) Dr Justin Malewezi, mwambowu umayanjanitsa Achewa ochokera m’maiko atatuwa. Dziko la Malawi ndilo lili ndi mafumu a Chichewa ambiri kuposa maiko enawa. Malawi ili ndi mafumu 136 a Achewa, pomwe ku Zambia aliko 36 pomwe ku Mozambique aliko 42.

Malewezi adati m’maboma onse a dziko la Malawi muli mafumu a Achewa, kupatula maboma a Balaka, Rumphi, Mzimba ndi Karonga.

M’maiko atatuwa muli Achewa 14 miliyoni, omwe 9 miliyoni mwa iwo akuchokera ku Malawi.

Nanga n’chifukwa chiyani mwambowu umachitikira ku Zambia osati ku Malawi komwe kuli mafumu komanso Achewa ochuluka?

Malewezi adayankha: “Mwambowu umachitikira komwe kuli likulu la Kalonga Gawa Undi. Pochokera ku Zaire kalekalelo, likulu la Achewa lidali ku Mankhamba ku Mtakataka m’boma la Dedza. Kenako lidasamukira ku Mozambique, koma kumeneko Apwitikizi amadana ndi mafumu ndipo Kalonga wanthawiyo adamangidwa kwa zaka 20. Atatulutsidwa, adasamukira ku Zambia komwe mpaka lero mwambowu umachitikira.”

Iye adafotokoza kuti Kalonga Gawa Undi ali ndi tanthauzo lakuya. Kalonga, akuchoka ku liwu lakuti kulonga chifukwa ali ndi mphamvu zolonga ufumu. Akutchedwa Gawa chifukwa ali ndi mphamvu yogawa malo; ndipo Undi chifukwa amateteza anthu ake.

Nanga chimachitika pamwambowu n’chiyani?

Mwambowu umakhala ukuchitika kwa sabata zingapo, koma umafika pachimake Loweruka lomaliza la mwezi wa Ogasiti. Patsikulo pamakhala magule osiyanasiyana ndipo mafumu a Chichewa amapereka mphatso kwa Kalongayo, kuthokoza. Apa ndipo pachokera mawu akuti kulamba.

“Mwambowu umachitika anthu atamaliza kukolola komanso akukonzekera mvula yotsatira. Mafumuwo amapereka mphatso kwa mfumuyo mothokoza. Komanso amaifotokozera momwe zinthu zilili m’maiko mwawo pankhani ya chakudya, matenda ndi zina zotero,” adatero Malewezi.

Chochititsanso chidwi patsikulo ndichakuti Kalonga Gawa Undi amakapereka moni kwa mayi ake Nyangu. Chinanso chochititsa chidwi udali mpando wachifumu umene Kalonga Gawa Undi adakhalapo, mozungulilidwa ndi asilikali ake komanso makhansala ake.

M’mbali mwa mpandowu mumayalidwa minyanga ya njovu. Ndipo kutsogolo kwake, mbali ya kumanzere kuli mutu wa kambuku, pomwe kumanja kuli mutu wa mkango. Izi zikusonyeza mphamvu ya mfumuyo poteteza anthu ake.

“Mwambowu udathetsedwa ndi atsamunda kwa zaka zambiri, kufikira m’chaka cha 1981 pomwe udayambikanso. Iyi ndi nthawi imene Achewa a m’maiko atatuwa amayanjana ndikusangalala za chikhalidwe chawo,” adatero Malewezi.

Pambali pa magule komanso mchezo, anthu adakhwasula nyama zosiyanasiyana za kuthengo kuphatikizapo njati.

Gule wamkulu adaliko mitundu yambiri, kuphatikizapo maria, makanja, nyolonyo, gologolo komanso chilembwe. Kudalinso magule ena monga manganje ndi soopa, utse komanso chisamba.

Related Articles

Back to top button
Translate »