Chichewa

Zochitika m’minibasi

Listen to this article

Tsikulo pa Wenela padalibe zomvera nyimbo. Nanga abale anzanga, anthu akuluakulu ngati ife tingamamvere nyimbo monga Tsika Msungwana Tsika? Nanga inu mungamvere nyimbo ija ya Msati Mseke. Za nyimbo imeneyi ndidamva kwa Gervazzio, amene akuti sangayerekeze kuika pamalo paja timakonda pa Wenela.

Amavala zigoba….Amadzipaka matope….

“Uku ndiye timati kufwala gule, kuulula vilombo. Adamuuza ndani kuti amachita kuvala? Kukadakhala kwathu ku Thiwi ku Nkhotakota, tikadacheza mwana uyu,” adatero Gervazzio.

art

Tsono tsiku limenelo kudali kuonera mafilimu a ku Nigeria. Pajatu ine mafilimu amenewa ndidaimika manja kalekale kuti sindidzaoneranso, amataitsa nthawi. Zoona filimu izikhala yoonetsa munthu akuliza galimoto, kudzaponda kuti vruuuu! Kenako kuyamba kuitana wapageti kuti akatsegule. Akatero wageti kulimbana ndi geti…. Kenako ndiye kuti muonera mphindi zisanu mkuluyo akuyendetsa galimoto….

Koma filimu imene tinkaonera tsikulo ndiyo yandichititsa kuti ndilekeretu kuonera filimuzi. Ngakhale wina atandithira Doom mkamwa, sindingachite. M’filimuyo mkazi wina adafuna kupha mwamuna wake kuti atenge chuma chake. Iye adaphika chakudya ndipo adathiramo tameki. Kuti adziwe kuti tamekiyo wakolera mayiyo adalawa chakudyacho!

Tsiku lotsatira, wa minibasi ina adati akufuna agwire ntchito ina ndipo adandipempha kuti ndiyendetse mmalo mwake. Ndidaima pa Wenela uku wina akuitanira. “Ndirande! Ndirande! Ndirande awiri a chamba! Awiri a change muno ku Ndirande!” adali kutero.

Nthawiyo nkuti ndikukhoma marivesi, kudzapititsa patsogolo pang’ono.

Mpando woyandikana ndi ine padakhala mkulu wina ndipo kuchitseko kudali msungwana wina amene anali ndi foni yake m’manja. Iye adali ndi chikwama chija amachitcha mwina ndi wokagona pamiyendo pake.

Chomwe chinkandichititsa chidwi chidali chakuti bamboo uja ankasunzumira zomwe msungwana amalemba pafonipo. Pena mzibamboyo amaseka nawo nkhani za msungwanayo. Ndikhulupirira idali Whatsapp imeneyo.

Mtsikana uja adaoneka kuti amanyansidwa ndi zochita za bamboo uja. Bamboyo adali kunjoya zolemba za msungwana uja.

Kenako, tikuyandikira pa Chimsewu mzibambo uja adayamba kukuwa. “Njoka! Njoka! Njoka!” adadumpha ndipo adachititsa kuti ndisiye chiwongolero. Pomwe ndimadzachigwiranso, nkuti minibasi ikutaya msewu.

“Mayo ine ngozi iyi! Ngozi iyi!” ena adali kukuwa.

“In the name of Jesus! In the name of Jesus!” enanso adali kukuwa.

Mwa chisomo, ndidakwanitsa kuimitsa minibasi ija. Padalibe wovulala. Koma bamboo uja adatsegula chitseko ngakhale adali pakati. Adamudumpha mstikana uja nkutuluka panja.

Adali kukuwa: “Njoka! Njoka! M’chikwama! Njoka!”

Msungwana uja adali kuseka chikhakhali.

“Bamboyu amawerenga mauthenga anga, ndiye ndimafuna asiye kuwerenga mauthenga a eni. Ndinangolemba uthenga uwu,” adatero akundiwerengetsa uthenga wopita kwa bwenzi lakewo.

Ndili m’minibasi koma abambo ndayandikana nawo akungowerenga mauthenga anga. Sakudziwa m’chikwamamu muli njoka.

Gwira bango! Upita ndi madzi!n

Related Articles

Back to top button
Translate »