Monday, May 23, 2022
  • About Us
  • ImagiNATION
  • Adverts
  • Rate Card
  • Contact Us
The Nation Online
Advertisement
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
No Result
View All Result
Home Chichewa

zofunika kulingalira potsegulira sukulu

by Steven Pembamoyo
22/08/2020
in Chichewa
4 min read
0
Share on FacebookShare on TwitterShare on WhatsAppShare on LinkedinLinkedinShare via Email

Miyezi 5 yatha tsopano ana asukulu ali pakhomo chifukwa cha mliri wa Covid-19. Iyi ndi nkhani yomwe yasautsa ndikuyimitsa mitu ya mikoko yogona. Masiku apitawa, mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera adati sukulu za m’dziko lino zikhonza kutsegulidwa mwezi wa mawa. Koma kadaulo pa nkhani zamaphunziro Steve Sharrah wati pali zofooka zoyenera kuziunikira pokonzekera kutsegulidwa kwa sukulu. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere:

Boma lati litsegula sukulu, ndikhulupilira ndinu okondwa ndi nkhaniyi?

Ndisakondwerenji ine munthu yemwe ndimayika mtima pa chilichonse chokhudza maphunziro. Maphunziro ndi wofunika kwambiri chifukwa amatsegula njira zambiri pamoyo wa munthu moti ngakhale chuma cha dziko chimayenda bwino ndi anthu ophunzira bwino. Ndidali mmodzi mwa anthu odandaula zedi momwe ana amangokhala pakhomo koma ndimamvetsetsa chifukwa Covid-19 siyidabwere bwino.

Sharra: Ndondomeko ikufunika

Mwanena nokha za Covid-19, kodi ndife okonzeka kutsegulira sukulu momwe wakulira mlili wa Covid-19?

Pamenepo mpamene pali nkhani yaikulu. Tikuyenera kusamala ndi kulingalira mofatsa potsegulira sukuluzi chifukwa tikhoza kudzikhwezanso tokha. Ndaona ndondomeko zomwe boma lakhazikitsa kuti litsatire potsegulira sukulu koma ndawonapo zofooka zingapo. Ngati munthu wokonda dziko lake, ndikuyamikira boma pa chidwi chake pa maphunziro koma mfundo ndiyimeneyi yoti mpofunika kusamala kuti ana ndi aphunzitsi asadzakhale pachiopsezo.

Akuti sukulu zitsegulidwe sabata yoyamba ya mwezi wa September, nzotheka zimenezi?

Ndikuona ngati tapupuluma panthawipo chifukwa pali zambiri zomwe zikuyenera kuchitika ana asukulu asadabwerere kusukuluko. Inu mukudziwa kuti sukulu zikuyenera kuunikidwa ngati zakwanitsa kutsata njira zopewera Covid-19 chifukwa kupanda kutero ndiye kuti ana ndi aphunzitsi ali pachiopsezo. Apa tikukamba za sukulu za pulaimale zokwana 6 300 komanso za sekondale 1 400 zofunika kuunikidwa pasabata ziwiri zokha, kupatula apo, sukuluzo zikuyenera kukhala ndi zipangizo zaukhondo monga zosambira m’manja kamanso pafunika mankhwala opopera m’sukuluzo. Zonsezi zifunika ndondomeko yogulira katundu m’boma ndipo ndondomekoyo imatenga nthawi kuti itheke tsono ndi nthawi yomwe ilipoyi ndikuwona ngati yachepa.

Tsono tikatengera lamulo lothandiza polimbana ndi Covid-19 makamaka pa chiwerengero chololedwa kukumana, zigwirizana ndi chiwerengero cha ana pasukulu?

Nkhani ina ndi imeneyo moti ndimaona ngati mpofunika kuti anawo agawidwe m’magulu angapo ndipo apatsidwe masiku opita kusukulu kokakumana ndi aphunzitsi pomwe masiku enawo azingopatsidwa ntchito yopangira pakhomo pa makolo awo. Ndikuona kuti njirayi ingathandize apo ayi palibe chomwe tikupanga chifukwa m’sukulu zina muli ana ambiri oti mwina ana kumafika 100 m’kalasi imodzi. Ngakhalenso matebulo omwe amagwiritsa ntchito adapangidwa za Covid-19 zisadaganiziridwe moti ophunzira amangotalikana pang’ono osafika mlingo omwe lamulo limanena. Pali zambiri zofunika kuunika ndithu.

Ena akuti makalasi akhale a panja kuti ana azitha kutalikana bwino. Muti chiyani?

Zimenezo ndaziona kale koma sizikuthandiza chilichonse chifukwa posachedwapa kuyamba mvula ndiye tidzakhalanso kakasi n’kumalingalira zotsekanso sukulu chifukwa cha nyengo ndiye tizingokhalira kutseka nkumati ana aphunziradi? Apapa titengerepo phunziro kuti tikamapanga mapulani tiziunikiratu zakutsogolo. Mwachitsanzo, kale lomwe lija tikadaganiza zomanga makalasi akuluakulu, tikadatero, bwenzi nkhani ya kuchuluka kwa ana m’kalasi isakutisautsa lero. Panopa tili ndi mwayi chifukwa tikupanga ndondomeko ya 2063 (Vision 2063) ndiye omwe akuona mbali yamaphunziro atigwilire ntchito yabwino apapa kuti vuto ili lisadzabukenso mtsogolo muno.

Nanga aphunzitsi ndi ana akonzekere motani?

Mbali ina ndi imeneyo ndiye muziwerengera kuti nawonso kukonzekera kwawo kuli m’sabata ziwiri zomwezo. Aphunzitsi akuyenera maphunziro apadera akapewedwe ka Covid-19 kuti azikatha kuunikira bwino ana komanso akayamba kuphunzitsa mundondomeko yachilendo. Aphunzitsi ali ndi ntchito yambiri yoti akwaniritse m’nthawi yochepa zomwenso akufunika kukonzekera mofatsa. Tikati tione za ana ndiye mavuto okhaokha chifukwa ana ambiri akuyenera thandizo loti mitu yawo imasuke. Pali ana ena oti adakhudzidwa ndi Covid-19 mwina kudzera mwa wachibale, ena akumana ndi nkhanza zosiyanasiyana pa miyezi yomwe adali pakhomo ndipo ena adatenga mimba kumene tsono onsewa sangangobwerera kusukulu lero nkumayembekezera kuti akapangako zakupsa.

Pakuoneka kuti mavuto ofunika kukonza achuluka, sitingangobwerera ku maphunziro a pa Intaneti kapena pawailesi?

Izonso ndiye zokanikazo. Maphunziro a pa Intaneti kapena wailesi ndi wokomera ana ochepa omwenso amachokera kochita bwino. Kwa ana ochokera m’mabanja osauka ndiye kuti tikuwaphera tsogolo. Mwachitsanzo, kalembera wa 2018 adapeza kuti mabanja 4 okha mwa mabanja 100 ndiwo amakwanitsa kukhala ndi mpata wa makina a computer kapena lamya yamakono kuwonyeza kuti ana ochokera mmabanja 96 sangapindule nawo pa maphunziro a pa internet. Kalembera yemweyo amasonyeza kuti anthu 16 mwa anthu 100 amakwanitsa kukhala ndi mpata wa internet tsono anthu ena otsalirawo tiwatani. Nkhani yaikulu apapa n’kukonzekera mokwanira basi.

Previous Post

Malingaliro Potsegulira sukulu

Next Post

Osangoti neba akuweta nkhumba

Related Posts

Nkhani

Agwidwa ndi yunifomu za polisi

May 22, 2022
Nkhani

Dollar yasowa

May 21, 2022
Foni kundende monga ya Zomba n’zoletsedwa
Nkhani

Apezeka ndi foni m’mimba

May 15, 2022
Next Post

Osangoti neba akuweta nkhumba

Opinions and Columns

People’s Tribunal

What was that press briefing all about?

May 22, 2022
Big Man Wamkulu

Wife, in-law plotting my downfall

May 22, 2022
My Thought

Tonse Alliance died on arrival

May 22, 2022
Layman's Reflection

New IMF programme pivotal moment for Tonse Alliance

May 21, 2022

Trending Stories

  • Musician Martse in hospital after fire accident

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Malawi overlooks players diet

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • How loans get wasted

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Gaba comes up with two options

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Onesimus leaves Major One Records

    0 shares
    Share 0 Tweet 0

Malawi-Music.com Top10

  • Values
  • Our Philosophy
  • Editorial policy
  • Advertising Policy
  • Code of Conduct
  • Plagiarism disclaimer
  • Disclaimer
  • Privacy Policy
  • Terms of use

© 2022 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation

© 2020 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

This website uses cookies. By continuing to use this website you are giving consent to cookies being used. Visit our Privacy and Cookie Policy.