Chichewa

Zokhudza mikangano ya ufumu

Listen to this article

 

Nkhani za ufumu zakhala zikuvuta kwa nthawi yaitali. Zina mwa nkhani zomwe zakhala zikupanga mitu ndi mikangano ya ufumu komanso pakati apo kudabuka ganizo loti m’matauni musamakhale mafumu STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Gulupu Santhe imodzi mwa mafumu akale.

Ndikudziweni mfumu.

Santhe: Makhoti asamalowererepo
Santhe: Makhoti asamalowererepo

Ndine Aclas Chisoni koma la ufumu ndine nyakwawa Santhe wa m’dera la T/A Kalolo ku Lilongwe.

Tiziti a Santhe ake ndi a ku Kasunguwa?

Chibale chilipo koma chakumizu. A ku Kasungu ndi a m’bere la a Nkhoma pomwe ife a kuLilongwe ndife a m’bere la a Mwale.

Ufumu mudaulowa liti?

Ndidalowa ufumu m’chaka cha 1985 achimwene anga a Wilson Pwela omwe adali afumu atamwalira m’chaka cha 1983. Panopa ndikutha zaka 21 ndili mfumu ndipo chaka chino ndikuyembekeza kukwenzedwa kufika pa Senior Group Santhe.

Pa zaka zonsezi mwakhala mfumu, ndi mavuto anji omwe mungatiuze kuti amapezeka mu ufumu?

Mavuto alipo ambiri osayiwala mikangano. Maufumu ambiri amatchuka ndi mikangano makamaka yemwe adali nfumu akamwalira ndiye kuti wina alowepo. Nthawi zina mpaka pamalowa za mankhwala kulimbirana ufumu. Vuto lina ndilakuti adani amachuluka chifukwa ukangoweruza mlandu, yemwe sizidamukomere basi chidani chimayamba pomwepo.

Ndiye pakatipo kudabuka zoti maufumu a mtauni athe, maganizo anu ngotani?

Sizowona ayi mafumu ndiwofunikabe paliponse. Chitukuko kuti chiyende ndi mafumu, pakagwa zovuta mafumu ndiwo amaongolera zonse. Palibe kanthu kuti ndi mtauni kapena kumudzi koma pomwe pali anthu pamayenera utsogoleri.

Makhansala sangagwire ntchito ya mafumu?

Inu tiyeni tiziganiza mozama. Mfumu amasankha munthu okhwima maganizo odziwa ndi kutsata mwambo ndi chikhalidwe tsono makhansala ambiri amasankhidwa kaamba ka maphunziro kapena kutha kulankhula basi. Utsogoleri wa ufumu sachita kampeni ayi anthu okha amaona kuti uyu atithandiza.

Nanga nkhani za ufumu kupititsa mukhoti?

Ukunso nkusokoneza chifukwa nkhani ya ufumu imayenera kukambidwa kumudzi apo ayi kwa DC ndipo zikavutitsitsa ku unduna wa zamaboma ang’onoang’ono ngati kholo la maufumu.

Munganeneponji pa zomwe anthu amakamba kuti mafumu ndi adyera komanso ziphuphu?

Choyamba zindikirani kuti mfumu ndi munthu ndiye anthu tidabadwa osiyanasiyana mitima. Zikhoza kutheka kuti alipo mafumu ena aziphuphu ndi adyera koma aliponso ena omwe kwawo nkutsogolera mudzi ndi anthu mwachilungamo ndiye fundo imeneyo ndi mutu waukulu kupangapo mtsutso.n

Related Articles

Back to top button
Translate »