Nkhani

Zokolola zichuluka

Unduna wa zamalimidwe wati chaka chino dziko la Malawi likolola chimanga chokwana matani 4.4 miliyoni chomwe nchopitilira mlingo omwe dziko lino limafuna pachaka wa matani 3.3 miliyoni.

Izi zikutanthauza kuti m’chakachi, m’dziko muno mukhala chakudya chokwanira ndi china chapadera chokwana matani 1.1 miliyoni.

Zikuoneka kuti anthu akolola chimanga chochuluka

Koma akadaulo ati boma likalekelera kuti bola alimi akolola zochuluka, sipatenga nthawi nkhani ya njala isadamveke.

Kadaulo pa zaulimi Tamani Nkhono Mvula wati m’zaka za mmbuyomo, chimanga chimakololedwa chokwana malingana ndi mlingo wa matani 3.3 miliyoni omwe amafunika pachaka koma chifukwa chosasamala, njala siyimachedwa kugwa.

“Vuto ndi loti alimi ambiri akamalima amatsogoza maganizo ogulitsa ndiye akangokolola kumakhala phwanyaphwanya kuyiwala kuti pakhomopo pafunikanso chakudya,” watero Nkhono Mvula.

Iye adati vuto lina ndi loti msika wa Admarc umachedwa kutsegulidwa ndipo izi zimapangitsa kuti chimanga chambiri agule ndi mavenda omwe ena amakagulitsa chimangacho kunja mwamseli.

“Chomwe chimachitika nchoti chimanga chakololedwa chochuluka ngati momwe tikuyembekezera chaka chinomu koma mmalo moti chikakhale ku nkhokwe za dziko, chambiri chimatuluka ndi mavenda chifukwa ndiwo amagula chambiri potengera chidodo cha Admarc,” watero Nkhono Mvula.

Mchaka cha 2019, m’dziko muno mudakololedwa chimanga chokwana matani 3.4 miliyoni kutanthauza kuti padali chapadera matani 0.1 miliyoni koma pakati pa July ndi September, anthu 670 000 adali atayamba kale kuvutika ndi njala.

Pofika miyezi ya pakati pa October 2019 ndi March 2020, anthu 1 060 000 adalibe chakudya chokwanira ndipo amadalira boma ndi mabungwe kuti adye.

Mu 2020, dziko la Malawi lidakolola chimanga chokwana matani  3.7 miliyoni kutanthauza kuti padali chapadera matani 0.4 miliyoni koma pofika pakati pa July ndi September, anthu 1 690 000 adali ndi njala.

Pakati pa October 2020 ndi March 2021, chiwerengerocho chidakwera kufika 2 620 000 ndipo akadaulo ati izi zimachitika chifukwa chopanda mapulani pokolola.

Nkhono Mvula adati alimi ndi ofunika maphunziro a zakadyedwe makamaka pa kuchuluka kwa chakudya chomwe munthu amafuna pachaka kuti azitha kusunga chokwanira.

Mkulu wa mgwirizano wamabungwe owona za malimidwe wa Civil Society Agriculture Network (Cisanet) Pamela Kuwali wati kupatula kuunikila alimi za mlingo wachakudya choyenera kusunga pabanja, Admarc ikuyenera kutsegula misika yake msanga.

“Admarc itatsegula msanga misika, ndiye kuti igula chimanga chokwanira chifukwa alimi azithamangira mtengo wabwino komanso zikhoza kupindulira alimi kwambiri,” watero Kuwali.

Mneneri wa unduna wa zamalimidwe Gracian Lunga wati undunawo wapanga ndondomeko yokhwima yofuna kuti boma lisunge chimanga chokwanira.

“Choyamba, Admarc ili chile kugula chimanga ndi mbeu zina, chachiwiri, ndimavenda okhawo omwe ali ndi chilolezo chogulira mbeu omwe aloledwe kugula komanso motsata mitengo ya boma,” watero Lungu.

Nduna ya zamalimidwe Lobin Lowe wakhala akunena kuti m’dziko muno mukhala chimanga chambiri ndi mbewu zina chifukwa cha ndondomeko ya zipangizo zotsika mtengo ya Affordable Inputs Programme (AIP) yomwe boma lidakhazikitsa.

Mupologalamuyi, alimi 4.2 million adalowa mubajeti ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo kuyerekeza ndi alimi 900 000 omwe adalowamo chaka chatha.

Related Articles

Back to top button