Nkhani

Zotsamwitsa pa kutseguliranso sukulu

Pomwe ana asukulu akuyembekezera kutsegulira sukulu, aphunzitsi akuti sadakonzeke zokaphunzitsa chifukwa boma silikuonetsa chidwi pa nkhawa zawo.

Mlembi wa bungwe la aphunzitsi la Teachers Union of Malawi (TUM) Charles Kumchenga wati aphunzitsi adapereka nkhawa zoti boma liwapangire sukulu zisadatsegulidwe koma mpaka lero palibe chomwe chikuoneka.

Kumchenga: Aphunzitsi adadandaula

Izi zikusemphana ndi zomwe mlembi wamkulu wa unduna wazamaphunziro Chikondano Musa wanena kuti undunawo wankonzeka mokwanira.

Koma kadaulo pa zamaphunziro Benedicto Kondowe wati mbali ziwirizi zipereke chithunzithunzi choyenera kwa Amalawi chifukwa njomba zikhoza kusokoneza makolo.

Makolo ena adandaula kale kuti kutsegulidwa kwa sukulu kwawapatsa chipsinjo chifukwa adali osakonzeka moti ngati boma silipeleka nthawi yokwanira yoperekera fizi, ana ambiri sapita.

“Apa ndalama yavuta kale ndi Covid-19, kupatula apo, atidzidzimutsa ndalama tilibe komabe tiyesetsa kukwereta kuti ana apite kusukulu,” watero Margaret Ausi wa ku Salima.

Bungwe la TUM lati lidagwirizana ndi boma kuti aphunzitsi apatsidwe ndalama zaukadziotche komanso maphunziro apadera ophunzitsira m’nyengo ya Covid-19.

“Potseka sukulu adati akuwopa kuti kusukulu kungafalitse Covid-19 kutanthauza kuti kusukulu n’koopsa ndiye pakufunika ndalama yaukadziotche,” watero Kumchenga.

Lachiwiri lapitali aphunzitsi adawopseza kuti ngati sapatsidwa ndalama yaukadziwotche, sayamba kuphunzitsa chifukwa nawo ndi anthu.

“Tikusiyana pati ndi ogwira ntchito kuchipatala ndi kupolisi omwe amalandira ndalama yaukadziwotche? Nafeso atipatse,” adatero aphunzitsi mukalata yomwe adapeleka ku unduna wa zamaphunziro.

Koma nduna yazamaphunziro Agness Nyalonje wati zonse zili mmalo sukulu zitsegulidwa Lolembali ndipo wati makolo atumize ana kusukulu.

“Sitingangobwera n’kumati tikutsegulira sukulu, takonzeka moti makolo atumize ana kusukulu,” watero Nyalonje.

Boma lidatseka sukulu pa 23 March 2020 malipoti oti Covid-19 yafika ku Malawi ndipo ana asukulu akhala pa tchuthi chosakonzekera kwa miyezi isanu.

Panyengoyi, ana ambiri makamaka asungwana atenga pathupi ndi kukwatiwa some zikutanthauza kuti maphunziro a ana oterewa asokonezeka.

Chiwerengero cha anthu opezeka ndi Covid-19 chidakwera kwambiri m’miyezi ya June ndi July koma pano chiwerengerocho chayamba kutsika ndipo boma lati likukhulupilira kuti Covid-19 itha.

Related Articles

Back to top button