Chichewa

‘Zulani mitengo ya fodya poopetsa matenda’

 

Nthawi ino alimi ambiri a fodya ali kalikiriki kufunafuna mbewu, kukonza malo omwe adzalimepo komanso kukonza ndi kufesa nazale.

Ngakhale izi zili choncho alimi ena m’maboma a Mzimba ndi Rumphi akutsalira pantchitoyi kaamba koti iwo sadazulebe mitengo ya fodya m’minda mwawo.

For better tobacco production, quality seeds are vital

Mlangizi wa za ulimi Lewick Zimba wauza Uchikumbe kuti izi zikhoza kudzaononga fodya munyengo ikubwerayi.

“Alimi amayenera kuzula ndi kuotcha mitengo imeneyi akangomaliza kuthyola fodya wawo kuti aphe tizilombo tonse tomwe tingakhale mumitengoyo.

“Fodya ali gulu limodzi ndi tomato ndi mbewu zina zomwe sizichedwa kugwidwa ndi matenda ndipo mitengo ija ikasiyidwa kwa nthawi yaitali m’munda umasanduka malo omwe tizilombo timasweranamo,”adatero Zimba.

Zimba adati madera amasiyana nyengo yokolola fodya. “Madera a kummwera ndi pakati amayenera kuyambirira kuzula pomwe madera a kumpoto amamalizira ngakhale nthawi yake madera onsewa ndi miyezi ya March mpaka April,” adatero Zimba.

Iye adati alimi omwe sadazule ndi kuotcha mitengo ya fodya m’minda mwawo akuyenra kutero nthawi ino ngati akufuna kudzapindula ndi fodya wawo nyengo ikudzayi.

“Fodya amafunika chisamaliro chokwanira ndipo chisamaliro chimenechi chimayamba mlimi akangokolola fodya wake m’munda,” adatero Zimba.

Iye adati alimi akuyenera kuzindikira zomwe akuyenera kuchita ndi nthawi yomwe akuyenera kutero kupewa kulakwitsa kapena kusokoneza zomwe zikadatha kupeweka.

“Alimi akuyenera kumvera alangizi komanso ngati apali zinthu zomwe sakumvetsetsa akuyenera kufunsa kwa alingizi a kudera lawo,” iye adatero.

Mlangiziyu adati Malawi ndi dziko lomwe limadalira ulimi wa fodya pobweretsa ndalama za kumaiko akunja kotero n’kofunika kuti fodya azisamalidwa bwino kuti phindu lake lizioneka pokhala kuti mbewuyi imafuna ntchito yambiri.

Amon Gondwe, mmodzi mwa alimi amene mpaka pano sanazulebe mitengo ya fodya m’boma la Rumphi, wati ntchito imawakulira kuti ayambe kuzula nthawi yomwe amaliza kuthyola fodya.

“Timati tidzazulabe kenaka mpaka kumapezeka kuti nthaka yauma ndipo mitengoyi imalimba ndiye timangozisiya,” adatero Gondwe.

Iye adati akudziwa za ubwino wozula mitego ya fodyayo akangomaliza kukolola, makamaka potengera kuti ntchito imachepa, koma kwina kumakhala kutayirira kumbali ya alimi, amene ambiri mwa iwo amafuna “adzipepese” kaye akangogulitsa fodya wawo.

Related Articles

Back to top button