Chichewa

Zungulizunguli mu Lilongwe

Listen to this article

Abale anzanga, inetu ukwati, nkhani ya ukwati, sindikamba nawo. Nkhani imeneyi, kwa ine ndimangoionera apo!!! Chifukwa chake nachi: Pali ana ena amene amaganiza kuti mayi awo ndi

amami, chonsecho mayi awo ndi anti. Komanso pali ana ena amene amaganiza kuti bambo awo ndi adadi chonsecho ndi ankolo.

art-police

Musayerekeze kundifunsa kuti ndikutanthauza chiyani chifukwa sindikuyankhani. Ndakwiya nanu chifukwatu ndili muno mu Lilongwe momwe ndimakumana ndi anyamata ena.

Musayerekezenso kundifunsa ngati nkhani yake inali ya ukwati kapena ayi. Mukadziwa mukufuna mutani?

Ndidatsika basi ya Lilongwe tsikulo chifukwa Abiti Patuma adandiuza kuti mzindawo uvuta.

Abale anzanga nanga nkadatani? Nkadachitanji chifukwatu ena adandiuza kuti uku nkwa gule ndipo ukwatiwo ndi wa abale.

Mwinatu sindidakuuzeni. Nthawi ija ankamanga ukwati anyamata aja, nthawi ya Moya Pete, ine ndidali pomwepo limodzi ndi Abiti Patuma.

Inde, anyamata aja adatchuka.

Chongoti mu Lilongwe fikeni, abale anzanga, inetu zikwama ndimachita kupanira ngati chiyani kaya!

Tidayenda kamtunda ndithu ndipo tidaona umo apolisi amatapira ndalama muno mu Lilongwe: Kwa Biwi, inde Lower Biwi! Kugonetsa abambo olemekezeka pansi ati vakabo yawatapula! Umo mu Devils Street, ati kumene chiwanda cha Satana chidafikira, asungwana kukopa abambo; anyamata kufwamba abambo ndipo ana kutoleza zimene ataya abambo.

Lilongwe iyooo!

Za kwinako sindikamba. Ati Kumpanda kwa Mafumu, inde ku Side kofikira Madonna; apa paakazembe ngakhalenso kumabedi ndiye eeeeh!

Nkhani ili apa ndi ya anyamata amene tidawapeza akuchita zawo. Musadandaule, aka si koyamba, komanso kumbukirani anyamata a mu Mchesimu tsiku lina adafuna kuphwanya hotela ati chifukwa mwini hotela adazembetsa ana ena!

Lilongwe iyooo!

Tsono nkhani yakula apa ndi yakuti Moya Pete tsono wakumana ndi zija adakumana nazo Mfumu Mose nthawi ija ankafunsidwa ngati Mustafa angasiyire mng’ono wake Ajibu mpando woyang’anira ife ojiya, osolola ndi osenza pano pa Wenela.

Tsono funso ilo adafunsa Abiti Patuma titadutsana ndi olanda mavenda, mizere ya galimoto muno mu Lilongwe-galimoto zina zogulidwa posolola paja-lidali lakuti: Koma Moya Pete izi azikwanitsa?

Gwira bango, upita ndi madzi mwaiwe. n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »