Nkhani

Amalawi akupereka maganizo pa zonyonga

Listen to this article

Komiti yoona zamalamulo m’Nyumba ya Malamulo ili mkati motolera maganizo aanthu pa zachilango chonyonga opezeka wolakwa pa milandu ya kupha, kuukira boma, kugwiririra ndi mirandu ina yoopsa.

Malingana ndi wapampando wa komitiyo a Peter Dimba, iwo azungulira m’zigawo zonse kutolera maganizowo ndipo ikamaliza komitiyo idzalemba lipoti lomwe lidzaperekedwe ku unduna wa zamalamulo.

Kodi chilango chonyonga chikhalepo, kapena ayi?

Lachiwiri lapitali komitiyo idakumana ndi mabungwe, mipingo, mafumu ndi anthu okhudzidwa m’chigawo chapakati ndipo maganizo a anthuwo adaonetsa kuti Amalawi sakuchifuna chilango chonyonga.

“Pa zomwe tatolerako kale m’chigawo chapakati zikusonyezeratu kuti anthu sakuchifuna chilango chimenechi ndipo chikuyenera kuchoka m’malamulo a dziko la Malawi,” adatero a Dimba.

Pa nkhawa zoti lamulolo likathetsedwa mchitidwe wophana, kugwiririra ndi kuukira boma ukhoza kuchuluka, a Dimba ati palibe umboni woti m’maiko momwe chilangocho chimagwira ntchito anthu saphwanya malamulo otere.

Pogwirizana nawo, womenyera anthu ufulu a Michael Kaiyatsa ati chilango chakupha chimangoonetsa kuipa mtima ndi nkhanza komanso kusalemekeza ufulu okhala ndi moyo.

“Chilango cha kupha si chilango chabwino ayi n’chonyazitsa umunthu. Chimaphwanya ndime 19 komanso 16 za malamulo a dziko lino. Anthu akuzunzika m’thupi ndi muuzimu polingalira kuti ali m’ndende komanso akudikira kuphedwa,” atero a Kaiyatsa.

Naye mkulu wa bungwe la Centre for Human Rights, Education, Advice and Assistance (Chreaa) a Victor Mhango ati anthu omwe ali m’ndende kudikira kuphedwa amaoneka a nkhope zaululu.

“Anthuwa akuzunzika kwambiri chifukwa amakhala kaye zaka akudikira kunyongedwa. Kuli bwino kuthetsa chilangochi n’kumangowagamula ndende ya moyo onse,” atero a Mhango.

Malingana ndi bungwe la Amnesty International, dziko la Malawi lidanyonga anthu komaliza m’chaka cha 1992 ndipo padakalipano anthu 27 ali m’ndende kudikira kunyongedwa.

Pa 28 April 2021 khoti lalikulu la Supreme Court of Appeal lidagamula kuti chilango chonyonga sichogwirizana ndi malamulo a dziko la Malawi chifukwa chimaphwanya lamulo la ufulu wokhala ndi moyo.

Related Articles

Back to top button