Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Gogo,

Ndili pa banja ndipo tili ndi mwana mmodzi. Koma vuto ndi loti anthu anawanamiza amuna anga kuti ndili ndi chibwenzi. Iwo adapita kwawo ndipo akuti sabwera mpaka aganize chochita.

Iwowotu ndi amene amachita zibwenzi. Kodi ndichite chiyani, ndidikire, kapena ndikasume?

SM,

Mulanje.

Zikomo SM,

Pajatu pali mawu akuti mamveramvera amapasula banja, izi zikuphelezera pa zimene zikukuonekerani. Lero banja lanu lili gwedegwede chifukwa amuna anu adamva kuti muli ndi chibwenzi.

Kunena zoona, amuna anuwo ali ndi kampeni kumphasa ndipo akungofuna musiyanepo basi. Mwina padakalipano ali mkati moyesa zida ndi mkazi amene akufuna kumukwatira.

Anthu amene amabisa zambiri amakhala pa chikaiko kwambiri ndi anzawo. Mwamuna wanuyo akuonetseratu kuti ndi wothothoka sidze, ndiye akuona ngati nanunso mumachita zibwenzi za mseri ngati iyeyo.

Apatu musachedwe, kasumeni kwa ankhoswe nu. Banja limene pali chikaiko ngakhalenso nsanje sililimba. Ngati sakukufunani akadangonena. Apapa akukutairani nthawi.

Tasemphana zipembedzo

Anatchereza,

Ndakhala pa banja zaka zitatu koma vuto ndi loti ine ndi mkazi wanga timapemphera zipembedzo zosiyana. Iye ndi msilamu ine ndi mkhristu ndipo zafika poti mwana kubadwa kumupatsa dzina la Chisilamu.

Sizimandisangalatsa ndipo ndikamuuza kuti anditsatire amakana n’kumati ana onse adzatsatire iyeyo. Ndithandizeni.

RK,

Lilongwe.

Zikomo RK,

Amene adayambitsa zoti anthu aziyamba akhala pa ubwenzi asanalowe m’banja adaopa zinthu ngati izi. Zoona anthu mungapezeke bwanji m’banja koma mukusemphana mipingo?

Ndikudziwa kuti mpingo wa munthu si maziko a chikondi. Ndaona mabanja opemphera mpingo umodzi kom akutha ngati masanje. Nthawi zinanso zimatheka kuti anthu a mipingo yosiyana kukhalira limodzi popanda vuto.

Izi zili apo, ndikuona kuti pachibwenzi mpomwe muyenera kugwirizana mmene nkhani ya chipembedzo idzakhalire. Ndaonapo mwamuna akutsatira mkazi kapena mkazi kutsatira mwamuna kapenanso aliyense kupitiriza kupemphera mpingo wake. Nthawi zina, aliyense amachoka mpingo wake ndipo onse amalawa mpingo wina limodzi.

Kupemphera mipingo yosiyana m’banja kumasonyeza kuti anthu simugwirizana kwenikweni. Tangoganizani mpingo umene mwamuna amapemphera umene umalola kudya nkhumba pomwe mkazi wake izi ndi zoletsedwa. Zizikhala bwanji?

Komanso mudziwe kuti kusiyana mipingo kumasokoneza ana. Iwotu amasowa omutsatira. Kambiranani ndipo unikirani bwino ndi mwachikondi za tsogolo la banja lanu kuti nkhani ya chipembedzo isasokoneze.

OFUNA MABANJA

Ndine mkazi wa zaka 30 ndipo ndikufuna mwamuna wa zaka 38. 0888066681

Ndikufuna mkazi wa zaka 19 mpaka 23. Ndili ndi zaka 24. 0884986626/0994278416

Ndine mnyamata wa zaka 27 ndipo ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 30 mpaka 40. 0888070065

Ndili ndi  zaka 32. Ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 18 mpaka 30. Akhale okonzeka kukayezetsa. 0888418065/0999315391

Ndidabadwa zaka 35 zapitazo ndipo ndikufuna mkazi wolekeza zaka 30 wa ku Thyolo. 096589616.

Related Articles

Back to top button
Translate »