Nkhani

Mabishopu akunena zoona—akadaulo

Listen to this article

Akatswiri pa nkhani za ndale adandaula ndi kusasintha kwa zinthu m’dziko lino kwa zomwe zakhala zikuchitika kwa zaka zambiri.

Mwa zina, kusasinthaku kukuoneka pa nkhani za katangale, kusiyana kwambiri pakati pa olemera ndi osauka, kusankhana mitundu, kulowa pansi kwa maphunziro komanso kulowa pansi kwa ntchito zaumoyo.

Mafuta akwera mtengo kwambiri

Mmodzi mwa akatswiriwa, a Makhumbo Munthali adayankhula izi mabishopu a chikatolika atatulutsa chikalata chawo pokumbukira kuti padutsa zaka 30 chilembereni chikalata chotchedwa kuti ‘Kukhala moyo m’chikhulupiliro chathu’ chomwe chidadzudzulanso boma panthawiyo.

M’chikalatachi chomwe chidatuluka Lamulungu, atsogoleri a mpingowo adandaulanso kuti utsogoleri wa Boma la Tonse ukufooka komanso kuti ukumachedwa kumanga mfundo ngakhale pali malamulo owalola kuchita zinthu m’nthawi yake, makamaka pa nkhani yolimbana ndi katangale.

“Tikukhulupirira kuti mtsogoleri wa dziko amene adaachita kampeni potsamira pamfundo yolimbana ndi katangale ndiponso amene adalonjeza kuti athana ndi vutoli, sayenera kuikira kumbuyo nduna ndi omuthandizira ake omwe akuganiziridwa kuti adatenga nawo mbali pankhani yokhudza mchitidwewu, makamaka pamene pali umboni wokwanira,” kalatayo ikutero.

A Munthali adati ndi chachidziwikire kuti ngakhale pali mbali zina zomwe tachita bwino, tikubwererabe mmbuyo monga dziko.

“Utsogoleri wathu komanso kusowa kwa chidwi chosintha zinthu, kusalikonda dziko, kuikira kumbuyo anthu akuba chuma cha boma, kukonderana anthu a mtundu umozi ndi zina zikulepheretsa kukwaniritsa zikhumbokhumbo za chikalata cha kukhala moyo m’chikhulupiliro chathu.

“Kalata yatsopanoyi idayenera kukhala yosangalalira kuti takwanitsa kufikira zolinga za kalata ya kukhala moyo m’chikhulupiliro chathu ya m’chaka cha 1992 koma ndi zachisoni kutengera madandaulo ochokera kwa ma Bishopu kuti zinthuzi sizidatheke,” adatero a Munthali.

Iwo adapempha utsogoleri wa mgwirizano wa Tonse kuti uchitepo kanthu pa zomwe atsogoleri a mpingo akuchita nazo nkhawa zi.

“Si koyamba anthu kudandaula za izi, anthu adandaulapo za mavuto amenewa m’magulu osiyanasiyana. Zinthuzi zikukhudza madandaulo osiyanasiyana omwe Amalawi ali nawo. Koma zikuoneka ngati boma likutenga nthawi kuchitapo kanthu kuti lithane ndi mavutowa.

“Boma likathana ndi mavutowa mmalo modikira atsogoleri a mpingo kuwakumbutsa kuti asamaikire kumbuyo adindo ochita katangale kapena kusawathandiza amene akulimbana ndi mchitidwewu,” iwo adatero.

Mneneri wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chomwe chikutsogolera mgwirizano wa Tonse mbusa Maurice Munthali adakana kuyankhapo pa nkhaniyi ponena kuti si koyenera kuti monga a chipani alowelere za kayendetsedwe ka boma koma mneneri wa boma ndi yemwe angayankhepo pa nkhaniyi.

Koma m’kuyankha kwawo, mneneri wa boma a Gospel Kazako adati ayankha kalatayo pambuyo akayiwerenga ndi kufotokoza zomwe boma lidakwanitsa kale kuchitako molingana ndi madandaulo omwe ali m’chikalatacho.

Iwo adatinso afotokoza zonse zomwe boma lili pafupi kuchita molingana ndi zomwe kalatayo yadandaulapo kuti Amalawi azikhala moyo wabwino.

“Kalatayo tayilandira ndi nsangala. Ife monga boma timatenga anzathu a mpingo wa Katolika ngati bwenzi lodalirika pankhani za chitukuko cha dziko lino, ndipo timalemekeza mawu ndi thandizo lawo,” adatero a Kazako.

Mfumu yaikulu Mwankhunikira ya ku Rumphi adavomereza kuti makamaka pankhani ya za chuma zinthu sizili bwino popeza anthu ambiri kuphatikizapo mafumuwo, malipiro awo akhala otsika kwa nthawi yaitali moti ndi mmene mitengo ya zinthu ikukwerera, sizikuyenda bwino.

“Kwa ife, utsogoleri wa Tonse uli bwinoko, koma anthu m’midzi akudandaula kwambiri ndi kukwera mtengo kwa zinthu monga mafuta a galimoto, mafuta ophikira, shuga, sopo, mchere ndi zinthu zina zofunikira pa moyo wa tsiku ndi tsiku choncho anthu osauka ku mudzi sakusangalala ndi moyo. Koma mwina popeza bomali ndi latsopano zinthu zikhoza kusintha mtsogolomu,” adatero amfumuwo.

Kuonjezera apo adandaulanso za kusowa kwa feteleza wotsika mtengo, kuti ngakhale anthu ali nazo ziphaso zogulira feterezayu, kufikira lero sadagulebe feterezayo ngakhale mvula yafika pachimake.

“Izi zikusonyeza kuti chaka chino kukhalanso njala popeza zokolola sizikhala zambiri kaamba koti anthu ambiri alephera kuthira feteleza m’nthawi yake,” adatero a Mwankhunikira.

Related Articles

Back to top button