Chichewa

‘Ndinkafuna mnyamata wamtali, wakuda’

Listen to this article

 Ubwenzi wa James Mdala ndi Asiyatu James unayamba pa September 22 2020, mumzinda wa Lilongwe. Awiriwo anali atakumana miyezi iwiri mmbuyo mwake.

James amagwira ntchito ngati dotolo wamkulu wa za mano pachipatala cha cha Kamuzu Central pomwe Asiyatu amagwira ntchito ya utolankhani pa wailesi ya Radio Islam.

“Pa chiyambi mayiwa anali mnzawo wa mnzanga, ndiye dzina lawo pokhala Asiyatu James, ine langa James Mdala, tidali ngati dad ndi daughter wake mpakana patadutsa miyezi iwiri, ndidapezeka ndawafunsira ubwenzi ndipo anandivomera,” analongosola James.

James akuti kupatula maonekedwe abwino a Asiyatu, anakopeka ndi makhalidwe ake.

Asiyatu ndi James adayamba ngati macheza

“Ndife a chipembezo cha Chisilamu ndipo chimalimbikitsa khalidwe labwino. Ndiye nditaona khalidwe lawo pa chipembezo komanso pa umunthu sindinachedwenso ayi koma kuwafunsira ubwenzi,” James adatero.

Pomwe Asiyatu anati mtima wake unagunda atakumana ndi James pomwe adapita kukamuona mnzake.

“Nditamuona, mtima wanga udagunda chifukwa cha maonekedwe ake omwe adandisangalatsa chifukwa ndi mnyamata wakuda ndi wamtali monga ndinkalotera,” adalongosola Asiyatu.

Iye adati awiriwo adayamba kucheza pambuyo pogawana nambala za foni ndipo zokamba za James zidali za chilungamo.

“Kudekha kwake, kukhulupirika komanso kudzichepetsa kwake zidandipatsa chikoka chifukwa ndi zomwe mtima wanga wakhala ukusakasaka. Kotero sindidachedwenso ndi kumutaitsa nthawi James ayi koma kumuvomera ubwenzi,” anatero Asiyatu.

Atakhala pa ubwenzi kwa chaka chimodzi, James ndi Asiyatu adadalitsa ukwati wawo pa 9 October 2021 pa mzikiti wa Wafa m’boma la Zomba ndipo adakasupira kuholo ya sekondale ya Malindi ku Zomba konko.

Iwo akulangiza achinyamata onse omwe adapeza mnzawo woti amange naye banja ndipo akhutitsidwa naye, kuti asachedwe koma adalitse mabanja awo.

“Kwa atsikana anzanga, chomwe ndingawalangize ndiye kuyedzamira mwa Mulungu basi popeza Iye ndi amene amamuongolera munthu kunjira yabwino yopezera mamuna kapena mkazi,” anatero Asiyatu.

Pomwe James amachokera m’mudzi mwa Chongo, Mfumu Chikowi, m’boma la Zomba, Asiyatu amachokera m’mudzi mwa Chilipa, Mfumu Chilipa m’boma la Mangochi.

Pakadalipano iwo akukhalira ku Area 10, mumzinda wa Lilongwe.

Related Articles

Back to top button